1 Samueli
1
Banja la Elikana
Panali munthu wina wochokera ku Ramataimu, Mzofimu wa ku dziko la mapiri la Efereimu. Iyeyu dzina lake anali Elikana ndipo anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu wa fuko la Efereimu. Iye anali ndi akazi awiri, Hana ndi Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe.
Chaka ndi chaka Elikana ankachoka ku mudzi kwawo kupita ku Silo kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Yehova Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi amene anali ansembe a Yehova. Tsiku lopereka nsembe likafika Elikana amapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi. Ngakhale ankamukonda Hana, koma ankamupatsa gawo limodzi popeza Yehova sanamupatse ana. Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa. Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe. Tsono mwamuna wake Elikana ankamufunsa kuti, “Hana ukulira chifukwa chiyani? Wakhumudwa ndi chiyani kuti sukufuna ndi kudya komwe? Kodi ine kwa iwe sindili woposa ana aamuna khumi?”
Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova. 10 Hana anavutika mʼmoyo mwake, ndipo anapemphera kwa Yehova akulira kwambiri. 11 Ndipo iye analumbira kuti, “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ngati muyangʼana kusauka kwa mtumiki wanune, ndi kuyankha pemphero langa osandiyiwala ine mtumiki wanu pondipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzamupereka mwanayo kwa inu Yehova masiku onse a moyo wake. Lumo silidzapita pa mutu pake.”
12 Akupemphera choncho kwa Yehova, Eli ankamuyangʼana pakamwa. 13 Hana ankapemphera chamumtima ndipo milomo yake inkangogwedera koma mawu ake samamveka. Choncho Eli anaganiza kuti anali ataledzera. 14 Ndipo anamufunsa Hana kuti, “Kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, ayambe wakuchokani vinyo mwamwayo.”
15 Koma Hana anayankha kuti, “Sichoncho mbuye wanga. Ndakhala ndikumukhuthulira Yehova chisoni changa. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa chilichonse, popeza nthawi yonseyi ndakhala ndikupereka kwa Yehova nkhawa yayikulu ndi mavuto anga. 16 Musaganize kuti mtumiki wanu ndi kukhala mkazi wachabechabe. Ine ndakhala ndi kupereka nkhawa yanga yayikulu ndi zowawa zanga.”
17 Eli anayankha, “Pitani mu mtendere, ndipo Mulungu wa Israeli akupatseni zimene mwamupemphazo.”
18 Hana anati, “Mundikomerebe mtima mtumiki wanune.” Kenaka anachoka nakadya, ndipo sanaonekenso wachisoni.
19 Elikana ndi banja lake anadzuka mmawa mwake nakapemphera pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anabwerera kwawo ku Rama. Elikana anakhala pamodzi ndi mkazi wake, ndipo Yehova anamukumbuka Hanayo. 20 Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.”
Hana Apereka Samueli kwa Yehova
21 Elikana ndi banja lake lonse anapita kukapereka nsembe ya pa chaka kwa Yehova ndi kukakwaniritsa malonjezo ake. 22 Koma Hana sanapite nawo popeza anawuza mwamuna wake kuti, “Mwanayu akadzaleka kuyamwa, ndidzapita naye ndi kukamupereka pamaso pa Yehova ndipo adzakhala kumeneko moyo wake wonse.”
23 Elikana mwamuna wake anamuwuza kuti, “Chita chimene chakukomera. Tsala kuno mpaka utamusiyitsa kuyamwa, Yehova yekha akwaniritse mawu ake.” Choncho mkaziyo anatsala ku nyumba ndi kusamalira mwana wake mpaka atamuletsa kuyamwa.
24 Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. 25 Tsono anapha ngʼombe yamphongo ija ndi kupereka mwana uja kwa Eli. 26 Ndipo Hana anati kwa Eli, “Mbuye wanga, ine ndikunenetsadi pamaso panu kuti ndine mkazi uja amene anayima pamaso panu ndi kumapemphera kwa Yehova. 27 Ndinapempha mwana uyu, ndipo Yehova wandipatsa chimene ndinamupempha. 28 Ndiye tsopano ine ndikumupereka kwa Yehova. Pa moyo wake wonse adzakhala wa Yehova.” Ndipo onse anapembedza Yehova kumeneko.