28
Ahazi Mfumu ya Yuda
Ahazi anali ndi zaka makumi awiri pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Iye sanachite zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide kholo lake. Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo anawumbanso mafano a chipembedzo cha Abaala. Iye amapsereza nsembe ku chigwa cha Hinomu, ndipo anaperekanso ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza kutsatira njira zonyansa za mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli. Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzerapo mafano, pamwamba pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu.
Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wake anamupereka mʼmanja mwa mfumu ya Aramu. Aaramu anamugonjetsa ndipo anagwira ukapolo anthu ake ambiri napita nawo ku Damasiko.
Yehova anamuperekanso mʼmanja mwa mfumu ya Israeli, imene inamuzunza ndi kumuphera anthu ake ambiri. Pa tsiku limodzi, Peka mwana wa Remaliya anapha asilikali 120,000 mu Yuda chifukwa Yuda anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo. Zikiri msilikali wa ku Efereimu, anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu woyangʼanira nyumba yaufumu, ndi Elikana wachiwiri kwa mfumu. Aisraeli anagwira ukapolo abale awo, akazi, ana aamuna ndi ana aakazi okwanira 200,000. Iwo anafunkhanso katundu wambiri amene anapita naye ku Samariya.
Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi, ndipo anapita kukakumana ndi gulu lankhondo pamene linabwerera ku Samariya. Iye anawawuza kuti, “Chifukwa Yehova, Mulungu wa makolo anu anakwiyira Ayuda, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Koma inu mwawapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba. 10 Ndipo tsopano mukufuna kuti amuna ndi akazi a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akhale akapolo anu. 11 Tsono mvereni! Abwezeni abale anu amene mwawagwira ukapolo, pakuti mkwiyo wa Yehova uli pa inu.”
12 Tsono atsogoleri ena a ku Efereimu, Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilayi anatsutsana nawo amene ankachokera ku nkhondo kuja. 13 Iwo anati, “Musabweretse akapolowo kuno, pakuti ife tidzakhala olakwa pamaso pa Yehova. Kodi mukufuna kuwonjezera pa machimo athu ndi kulakwa kwathu? Pakuti zolakwa zathu ndi zambiri kale ndipo mkwiyo wake woopsa uli pa Israeli.”
14 Kotero asilikali aja anawasiya akapolowo pamodzi ndi katundu amene analanda ku nkhondo pamaso pa akuluakulu ndi gulu lonse la anthu. 15 Anthu amene atchulidwa mayina aja anatenga akapolowo, ndipo kuchokera pa zolanda ku nkhondo, anawaveka onse amene anali maliseche. Anawapatsa zovala ndi nsapato, chakudya ndi chakumwa ndi mankhwala. Onse amene anali ofowoka anawakweza pa abulu. Choncho anabwera nawo kwa abale awo ku Yeriko, Mzinda wa Migwalangwa, ndipo kenaka anawabweza ku Samariya.
16 Pa nthawi imeneyo mfumu Ahazi inatumiza mawu kwa mfumu ya ku Asiriya kupempha chithandizo. 17 Ankhondo a ku Edomu anabweranso ndi kuthira nkhondo Yuda ndi kugwira akapolo. 18 Pamenepo nʼkuti Afilisti atathira nkhondo mizinda ya mʼmbali mwa phiri ndi ku Negevi ku Yuda. Iwo analanda mizindayo nakhala ku Beti-Semesi, Ayaloni ndi Gederoti, komanso Soko, Timna ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. 19 Yehova anapeputsa Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi ya Israeli, pakuti analimbikitsa zoyipa ku Yuda ndipo anali munthu wosakhulupirika kwambiri pamaso pa Yehova. 20 Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera kwa iye, ndipo anabweretsa mavuto mʼmalo momuthandiza. 21 Ahazi anatenga zinthu zochokera mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba yaufumu ndi kwa atsogoleri ndipo anazipereka kwa mfumu ya ku Asiriya, koma zimenezo sizinamuthandize.
22 Pa nthawi yake yamavutoyi mfumu Ahazi inapitirira kukhalabe yosakhulupirika pamaso pa Yehova. 23 Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse.
24 Ahazi anasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse kuchokera mʼNyumba ya Mulungu ndipo anazitenga. Iye anatseka zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anayimika maguwa ansembe pa ngodya iliyonse ya msewu mu Yerusalemu. 25 Mu mzinda uliwonse wa Yuda anamangamo malo achipembedzo, operekerapo nsembe zopsereza kwa milungu ina ndipo anaputa mkwiyo wa Yehova, Mulungu wa makolo ake.
26 Zochitika zina pa ulamuliro wake ndi machitidwe ake onse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 27 Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sanamuyike mʼmanda a mafumu a Israeli. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.