KALATA YACHIWIRI YA PAULO YOLEMBERA
AKORINTO
1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi mʼbale wathu Timoteyo,
Kulembera mpingo wa Mulungu mu Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse mu Akaya monse.
Mukhale ndi chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
Mulungu Mwini Chitonthozo
Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu. Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri. Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife. Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi.
Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo. Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa. 10 Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe. 11 Mutithandize potipempherera. Pamenepo ambiri adzathokoza mʼmalo mwathu, chifukwa cha chisomo chake poyankha mapemphero a anthu ambiri.
Paulo Afotokoza za Kusintha kwa Ulendo Wake
12 Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu. 13 Pakuti sitikukulemberani zoti simungawerenge kapena kumvetsetsa. 14 Monga mwamva pangʼono chabe, ndikuyembekeza kuti mudzamvetsa kwenikweni, kuti mutha kutinyadira monga ife tidzakunyadirani, pa tsiku la Ambuye Yesu.
15 Popeza ndinatsimikiza mtima za ichi, nʼchifukwa chake ndinafuna kuti poyamba, ndidzakuchezereni kuti mupindule pawiri. 16 Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya. 17 Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?”
18 Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.” 19 Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.” 20 Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu. 21 Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife, 22 nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.
23 Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni. 24 Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.