2
Aphunzitsi Onyenga
Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi. Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira.
Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo. Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu. Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa. (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva). Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. 10 Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro.
Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba. 11 Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye. 12 Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa.
13 Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo. 14 Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa! 15 Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama. 16 Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo.
17 Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani. 18 Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa. 19 Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira. 20 Ngati anapulumuka ku zodetsa za dziko lapansi podziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, pambuyo pake nagwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zomwezo, potsiriza adzakhala oyipa kuposa mmene analili poyamba. 21 Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa. 22 Kwa iwo miyambi iyi ndi yoona, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndipo, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhunizikanso mʼmatope.”