2 Samueli
1
Davide Amva za Imfa ya Sauli
Atamwalira Sauli, Davide anabwerako kumene anakagonjetsa Aamaleki ndipo anakakhala ku Zikilagi masiku awiri. Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo.
Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.”
Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?”
Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.”
Ndipo Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa nkhaniyi, “Ukudziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?”
Mnyamatayo anati, “Zinangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa, ndipo Sauli anali komweko ataweramira pa mkondo wake, pamodzi ndi magaleta ndi okwera ake atamuyandikira. Pamene anatembenuka ndi kundiona ine, iye anandiyitana, ndipo ndinati, ‘Kodi ndichite chiyani?’ ”
Iye anandifunsa, “Iwe ndiwe yani?”
Ine ndinayankha kuti, “Ndine Mwamaleki.”
“Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’
10 “Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.”
11 Apo Davide ndi anthu onse amene anali nawo anangʼamba zovala zawo. 12 Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga.
13 Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa uthengawo, “Iwe umachokera kuti?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndine mwana wa mlendo Mwamaleki.”
14 Davide anamufunsanso kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunaope kukweza dzanja lako ndi kupha wodzozedwa wa Yehova?”
15 Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa. 16 Pakuti Davide anali atanena kwa iye kuti, “Iwe wadzipha wekha. Pakamwa pako pakunena zokutsutsa wekha, pamene unanena kuti, ‘Ine ndapha wodzozedwa wa Yehova.’ ”
Davide Alira Maliro a Sauli ndi Yonatani
17 Davide anayimba nyimbo iyi ya maliro, kulira Sauli ndi mwana wake Yonatani. 18 Ndipo analamula kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimbo ya maliroyi imene yalembedwa mʼbuku la Yasari:
19 “Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda.
Taonani amphamvu agwa kumeneko!
 
20 “Musakanene zimenezi ku Gati,
musazilengeze ku misewu ya ku Asikeloni,
kuti ana aakazi a Afilisti angasangalale,
ana aakazi a osachita mdulidwe angakondwere.
 
21 “Inu mapiri a ku Gilibowa,
musakhalenso ndi mame kapena mvula,
kapena minda yobereka zopereka za ufa.
Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa,
chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta.
 
22 “Pa magazi a ophedwa,
pa mnofu wa amphamvu,
uta wa Yonatani sunabwerere,
lupanga la Sauli silinabwere chabe.
 
23 “Sauli ndi Yonatani,
pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima,
ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe.
Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga,
anali ndi mphamvu zoposa mkango.
 
24 “Inu ana aakazi a Israeli,
mulireni Sauli,
amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa,
amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide.
 
25 “Taonani amphamvu agwa ku nkhondo!
Yonatani wagona ataphedwa ku zitunda.
26 Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani,
unali wokondedwa kwambiri kwa ine.
Chikondi chako pa ine chinali chopambana,
chopambana kuposa chikondi cha akazi.
 
27 “Taonani amphamvu agwa!
Zida zankhondo zawonongeka!”