13
Amnoni ndi Tamara
Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola.
Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye.
Koma Amnoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu mwana wamwamuna wa Simea, mʼbale wake wa Davide. Yonadabu anali munthu wochenjera kwambiri. Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?”
Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.”
Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.”
Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.”
Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.” Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo. Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana.
Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka. 10 Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake. 11 Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.”
12 Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere. 13 Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.” 14 Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira.
15 Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!”
16 Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.”
Koma anakana kumumvera. 17 Amnoni anayitana wantchito wake ndipo anati, “Mutulutse mkazi uyu muno ndipo utseke chitseko akatuluka.” 18 Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala. 19 Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita.
20 Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa.
21 Mfumu Davide itamva zimenezi, inakwiya kwambiri. 22 Abisalomu sananene mawu aliwonse kwa Amnoni; abwino kapena oyipa. Iye anamuda Amunoniyo chifukwa anachititsa manyazi mlongo wake Tamara.
Abisalomu Apha Amnoni
23 Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko. 24 Abisalomu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Ometa nkhosa za mtumiki wanu anabwera. Chonde mfumu ndi akuluakulu anu mubwere kudzakhala nane?”
25 Mfumu inayankha kuti, “Ayi mwana wanga, tisapite tonsefe. Tidzakhala cholemetsa kwa iwe.” Ngakhale Abisalomu anayesetsa kuwumiriza mfumuyo, inakana kupita. Mʼmalo mwake inangomudalitsa Abisalomuyo.
26 Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.”
Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?” 27 Koma Abisalomu anamuwumiriza, kotero analola kuti Amnoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye.
28 Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.” 29 Kotero antchito a Abisalomu anachita kwa Amnoni zimene Abisalomu anawalamula. Kenaka ana onse a mfumu anayimirira ndipo anakwera pa abulu awo nathawa.
30 Ali mʼnjira, Davide anamva mphekesera yakuti, “Abisalomu wakantha ana onse a mfumu ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala.” 31 Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo.
32 Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara. 33 Mbuye wanga mfumu musavutike ndi maganizo ndi nkhani yoti ana onse a mfumu afa. Wafa ndi Amnoni yekha.”
34 Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa.
Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.”
35 Yehonadabu anati kwa mfumu, “Taonani ana a mfumu afika. Zachitika monga momwe mtumiki wanu ananenera.”
36 Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa.
37 Abisalomu anathawa, napita kwa Talimai mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Koma mfumu Davide inalira mwana wake tsiku ndi tsiku.
38 Abisalomu atathawa ndi kupita ku Gesuri, anakhala kumeneko zaka zitatu. 39 Ndipo Davide anagwidwa ndi chifundo chofuna kumulondola Abisalomu pakuti anali atatonthozedwa pa imfa ya Amnoni.