20
Seba Awukira Davide
1 Ndipo munthu wina wokonda kuyambitsa chisokonezo, dzina lake Seba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini, anali komweko. Iye analiza lipenga ndipo anafuwula kuti,
“Ife tilibe chathu mu mfumu wa Davide,
tilibe gawo mwa mwana wa Yese!
Inu Aisraeli aliyense apite ku nyumba kwake!”
2 Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu.
3 Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye.
4 Kenaka mfumu inati kwa Amasa, “Itanitsa ankhondo a Yuda kuti abwere kwa ine pasanathe masiku atatu, ndipo iwe udzakhale nawo.” 5 Motero Amasa anakayitana Ayuda, koma anachedwa, napitirira pa nthawi imene mfumu inamuyikira.
6 Davide anati kwa Abisai, “Tsono Seba mwana wa Bikiri adzatipweteka kuposa momwe Abisalomu anatichitira. Tenga asilikali a mbuye wako ndipo umuthamangitse, mwina adzapeza mizinda yotetezedwa ndi kutithawa ife.” 7 Kotero anthu a Yowabu, Akereti ndi Apeleti ndiponso asilikali onse amphamvu anapita motsogozedwa ndi Abisai. Iwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri.
8 Ali pa mwala waukulu wa ku Gibiyoni, Amasa anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala chovala chausilikali ndipo pamwamba pa malayawo, mʼchiwuno mwake anavala lamba womangirirapo lupanga lili moyikamo mwakemo. Akuyenda linasololoka kuchoka moyikamo mwake.
9 Yowabu anati kwa Amasa, “Kodi uli bwanji mʼbale wanga?” Kenaka Yowabu anamugwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja ndi kupsompsona. 10 Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri.
11 Mmodzi mwa ankhondo a Yowabu anakayimirira pafupi ndi mtembo wa Amasa ndipo anati, “Aliyense amene amakonda Yowabu ndi aliyense amene ali wa Davide, atsatire Yowabu!” 12 Amasa anagona pakati pa msewu atasamba magazi ake, ndipo munthuyo anaona kuti asilikali onse amayima pamenepo. Atazindikira kuti aliyense amene ankafika pamene panali Amasa amayima, iye anamuchotsa mu msewu ndi kumukokera mʼmunda ndipo anamuphimba ndi nsalu. 13 Amasa atachotsedwa pa msewu anthu onse anapita ndi Yowabu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri.
14 Seba anadutsa mafuko onse a Israeli mpaka ku Abeli ndi Beti-Maaka ndiponso chigawo chonse cha Abeli, amene anasonkhana pamodzi ndi kumutsata iye. 15 Ankhondo onse pamodzi ndi Yowabu anafika ndi kumuzungulira Seba mu Abeli-Beti-Maaka. Iwo anapanga mzere wa nkhondo mpaka ku mzinda, ndipo unayangʼanana ndi malo otetezera a kunja. Pamene amalimbana ndi khoma kuti aligwetse, 16 mayi wina wanzeru anafuwula kuchokera mu mzindawo, “Tamverani! Tamverani! Muwuzeni Yowabu abwere pano kuti ndiyankhule naye.” 17 Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?”
Iye anayankha kuti, “Ndine.”
Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.”
Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.”
18 Iye anapitiriza kunena kuti, “Kalekale ankanena kuti, ‘Kapeze yankho lako ku Abeli,’ ndipo nkhani imathera pamenepo. 19 Ife ndife anthu a mtendere ndi okhulupirika mu Israeli. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene ndi mayi mu Israeli. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufafaniza cholowa cha Yehova?”
20 Yowabu anayankha kuti, “Ayi ndisatero. Ine sindikufuna kuwufafaniza kapena kuwuwononga. 21 Nkhani simeneyo ayi. Koma munthu wina wa ku dziko lamapiri la Efereimu, dzina lake Seba mwana wa Bikiri, wawukira mfumu Davide. Muperekeni munthuyo ndipo ine ndidzachoka pa mzinda uno.”
Mayiyo anati kwa Yowabu, “Mutu wake tikuponyerani pa khoma pano.”
22 Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu.
23 Yowabu ndiye amalamulira gulu lonse la ankhondo. Benaya mwana wa Yehoyada amalamulira Akereti ndi Apeleti. 24 Adoramu amayangʼanira anthu ogwira ntchito ya thangata, Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika, 25 Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiatara anali ansembe 26 ndipo Ira wa ku Yairi anali wansembe wa Davide.