4
Atsutsa za Kumanganso Nyumba ya Yehova
Adani a Yuda ndi Benjamini anamva kuti anthu obwera ku ukapolo aja akumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.”
Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.”
Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo. Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo.
Kutsutsa Kwina pa Nthawi ya Ahasiwero ndi Aritasasita
Mfumu Ahasiwero atangoyamba kulamulira dzikolo, adani aja analemba kalata yoneneza anthu a Yuda ndi Yerusalemu.
Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.
Rehumu mkulu wankhondo ndi Simisai mlembi, nawonso analemba kalata yawo yoneneza anthu a ku Yerusalemu kwa mfumu Aritasasita. Anayilemba motere:
Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu, 10 ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate.
11 Mawu a mʼkalata ya kwa Aritasasita anali awa:
Kwa mfumu Aritasasita:
Kuchokera kwa atumiki anu, anthu a kutsidya kwa Yufurate:
 
12 Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko.
13 Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa. 14 Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse. 15 Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga. 16 Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.
17 Mfumu inatumiza yankho ili:
Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate.
Landirani moni.
 
18 Kalata imene munatumiza ija yawerengedwa bwino lomwe pamaso panga. 19 Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo. 20 Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse. 21 Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula 22 Musachedwe kuchita zimenezi. Kodi ine ndingalole bwanji kuti zowononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?
23 Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo.
 
24 Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.