5
Mibado Kuyambira pa Adamu Mpaka Nowa
Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi:
 
Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”
Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.
Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.
Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani. 10 Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 11 Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.
12 Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli. 13 Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.
15 Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi. 16 Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 17 Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira.
18 Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki. 19 Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 20 Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira.
21 Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela. 22 Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 23 Zaka zonse za Enoki zinali 365. 24 Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.
25 Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki. 26 Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 27 Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.
28 Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29 Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.” 30 Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 31 Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
32 Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.