22
Kuyesedwa kwa Abrahamu
1 Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!”
Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”
2 Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.”
3 Abrahamu anadzuka mmamawa wake namangirira chokhalira pa bulu. Atadula nkhuni zokwanira zowotchera nsembe yopsereza, Abrahamu, antchito ake awiri pamodzi ndi Isake ananyamuka kupita kumalo kumene Mulungu anamuwuza Abrahamu. 4 Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. 5 Ndipo Abrahamu anati kwa antchito ake aja, “Bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, koma tibweranso.”
6 Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, 7 Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?”
Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.”
Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?”
8 Abrahamu anayankha, “Mwana wanga, Mulungu adzipezera yekha mwana wankhosa wa nsembe yopsereza.” Ndipo awiriwo anapitiriza ulendo.
9 Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja. 10 Kenaka Abrahamu anatambasula dzanja lake natenga mpeni kuti aphe mwana wake. 11 Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!”
Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”
12 Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
13 Abrahamu anatukula maso ake ndipo anaona nkhosa yamphongo itakoledwa ndi nyanga zake mu ziyangoyango. Iye anapita nakatenga nkhosa ija ndikuyipha ngati nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake. 14 Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.”
15 Mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba kachiwiri 16 ndipo anati, “Ndikulumbira mwa Ine ndekha kuti popeza wachita zimenezi, wosandikaniza mwana wako mmodzi yekhayu, 17 ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengalenga komanso ngati mchenga wa mʼmphepete mwa nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo, 18 ndipo kudzera mwa chidzukulu chako, mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi idzadalitsika, chifukwa iwe wandimvera.”
19 Kenaka Abrahamu anabwerera kumene anasiya antchito ake kuja nanyamukira nawo pamodzi kupita ku Beeriseba. Ndipo Abrahamu anakhala ku Beeriseba.
Ana Aamuna a Nahori
20 Patapita nthawi, Abrahamu anamva kuti, “Milika nayenso anaberekera Nahori, mʼbale wake ana. 21 Woyamba anali Huzi ndipo kenaka mʼbale wake Buzi. Anaberekanso Kemueli, amene anali abambo ake a Aramu. 22 Ana ena ndi Kesede Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betueli.” 23 Betueli anabereka Rebeka. Milika anaberekera Nahori, mʼbale wake wa Abrahamu, ana aamuna asanu ndi atatu amenewa. 24 Mkazi wake wachiwiri, dzina lake Reuma, anamubaliranso Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.