KALATA YOLEMBERA
AHEBRI
1
Khristu Mwana wa Mulungu Aposa Angelo
Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.
Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati,
“Iwe ndiwe mwana wanga;
Ine lero ndakhala Atate ako.”
Kapena kunenanso kuti,
“Ine ndidzakhala abambo ake;
iye adzakhala mwana wanga.”
Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati,
“Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”
Iye ponena za angelo akuti,
“Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo,
amasandutsa atumiki ake malawi amoto.”
Koma za Mwana wake akuti,
“Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya,
ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.
Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
Nʼchifukwa chake, Mulungu wanu wakukwezani kuposa anzanu
pokudzozani mafuta osonyeza chimwemwe.”
10 Mulungu akutinso,
“Ambuye, pachiyambi Inu munayika maziko a dziko lapansi;
ndipo zakumwambako ndi ntchito za manja anu.
11 Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu wachikhalire.
Izo zidzatha ngati zovala.
12 Mudzazipindapinda ngati chofunda;
ndipo zidzasinthidwa ngati chovala.
Koma Inu simudzasintha,
ndipo zaka zanu sizidzatha.”
13 Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti,
“Khala kudzanja langa lamanja
mpaka nditapanga adani ako
kukhale chopondapo mapazi ako.”
14 Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?