30
Tsoka kwa Mtundu Wopanduka
Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira
amene amachita zowakomera iwo okha osati Ine,
nachita mgwirizano wawowawo
koma osati motsogozedwa ndi Ine.
Choncho amanka nachimwirachimwira.
Amapita ku Igupto kukapempha thandizo
koma osandifunsa;
amathawira kwa Farao kuti awateteze,
ku Igupto amafuna malo opulumulira.
Koma chitetezo cha Farao chidzakhala manyazi anu,
malo a mthunzi a ku Igupto mudzachita nawo manyazi.
Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani,
ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi,
aliyense wa ku Yuda adzachita manyazi
chifukwa cha anthu opanda nawo phindu,
amene sabweretsa thandizo kapena phindu,
koma manyazi ndi mnyozo.”
Uthenga wonena za nyama za ku Negevi:
Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa,
mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi,
mphiri ndi njoka zaululu.
Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo,
kupita nazo kwa mtundu wa anthu
umene sungawathandize.
Amapita ku Igupto amene thandizo lake ndi lachabechabe.
Nʼchifukwa chake dzikolo ndalitcha
Rahabe chirombo cholobodoka.
 
Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita,
ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuona
ndipo lidzakhala ngati umboni wosatha
masiku a mʼtsogolo.
Amenewa ndi anthu owukira, onama ndi
osafuna kumvera malangizo a Yehova.
10 Iwo amawuza alosi kuti,
‘Musationerenso masomphenya!’
Ndipo amanena kwa mneneri kuti,
‘Musatinenerenso zoona,’
mutiwuze zotikomera,
munenere za mʼmutu mwanu.
11 Patukani pa njira ya Yehova,
lekani kutsata njira ya Yehova;
ndipo tisamvenso mawu
a Woyerayo uja wa Israeli!”
12 Nʼchifukwa chake Woyerayo wa Israeli akunena kuti,
“Popeza inu mwakana uthenga uwu,
mumakhulupirira zopondereza anzanu
ndipo mumadalira kuchita zoyipa,
13 choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalu
pa khoma lalitali ndi lopendama
limene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga.
14 Lidzaphwanyika ngati mbiya
imene yanyenyekeratu,
mwakuti pakati pake sipadzapezeka phale ngakhale
lopalira moto mʼngʼanjo
kapena lotungira madzi mʼchitsime.”
15 Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi:
“Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka,
ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu,
koma inu munakana zimenezi.
16 Inu mukuti, ‘Ayi ife tidzathawa,
tidzakwera pa akavalo aliwiro.’
Zoonadi kuti mudzakwera pa akavalo aliwiro,
koma okuthamangitsani adzakhalanso aliwiro.
17 Anthu 1,000 mwa inu adzathawa
poona mdani mmodzi;
poona adani asanu okha
nonsenu mudzathawa.
Otsala anu
adzakhala ngati mbendera pa phiri,
ndi ngati chizindikiro cha pa chulu.”
 
18 Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
19 Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani. 20 Ngakhale Ambuye adzakulowetseni mʼmasautso, aphunzitsi anu sadzakhala kakasi; inu mudzawaona ndi maso anuwo. 21 Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.” 22 Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”
23 Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka. 24 Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo. 25 Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono. 26 Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.
27 Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali,
ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka.
Iye wayankhula mwaukali kwambiri,
ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka.
28 Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira,
wa madzi ofika mʼkhosi.
Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza;
Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo,
kuti ziwasocheretse.
29 Ndipo inu mudzayimba
mokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika.
Mudzasangalala
ngati anthu oyimba zitoliro
popita ku phiri la Yehova,
thanthwe la Israeli.
30 Anthu adzamva liwu la ulemerero la Yehova
ndipo adzaona dzanja lake likutsika pa iwo
ndi mkwiyo woopsa, pamodzi ndi moto wonyeketsa,
mphenzi, namondwe ndi matalala.
31 Asiriya adzaopa liwu la Yehova,
ndipo Iye adzawakantha ndi ndodo.
32 Yehova akamadzalanga adani ake ndi ndodo,
anthu ake adzakhala akuvina nyimbo
zoyimbira matambolini ndi azeze,
Yehova ndiye ati adzamenyane ndi Asiriyawo.
33 Malo otenthera zinthu akonzedwa kale;
anakonzera mfumu ya ku Asiriya.
Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu,
ndipo muli nkhuni zambiri;
mpweya wa Yehova,
wangati mtsinje wa sulufule,
udzayatsa motowo pa nkhunizo.