6
Kuzingidwa kwa Yerusalemu 
  1 “Thawani, inu anthu a ku Benjamini!  
Tulukani mu Yerusalemu!  
Lizani lipenga ku Tekowa!  
Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!  
Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,  
ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.   
 2 Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,  
kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?   
 3 Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo;  
adzamanga matenti awo mowuzinga,  
ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”   
 4 Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo!  
Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano.  
Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka,  
ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.   
 5 Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno  
ndi kuwononga malinga ake!”   
 6 Yehova Wamphamvuzonse akuti,  
“Dulani mitengo  
ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.  
Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;  
wadzaza ndi kuponderezana.   
 7 Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi  
ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.  
Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;  
nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.   
 8 Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,  
kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere  
ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja  
mopanda munthu wokhalamo.”   
 9 Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti,  
“Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli,  
monga momwe amachitira populula mphesa.  
Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe  
monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”   
 10 Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?  
Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?  
Makutu awo ndi otsekeka  
kotero kuti sangathe kumva.  
Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;  
sasangalatsidwa nawo.   
 11 Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,  
ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova.  
Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu  
ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;  
pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,  
pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.   
 12 Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,  
pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.  
Ndidzatambasula dzanja langa kukantha  
anthu okhala mʼdzikomo,”  
akutero Yehova.   
 13 “Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,  
onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;  
aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,  
onse amachita zachinyengo.   
 14 Amapoletsa zilonda za anthu anga  
pamwamba pokha.  
Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’  
pamene palibe mtendere.   
 15 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo?  
Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe;  
sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe.  
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;  
adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,”  
akutero Yehova.   
 16 Yehova akuti,  
“Imani pa mphambano ndipo mupenye;  
kumeneko ndiye kuli njira zakale,  
funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,  
ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.  
Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’   
 17 Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni  
ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’  
koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’   
 18 Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;  
yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,  
chimene chidzawachitikire anthuwo.   
 19 Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,  
ndikubweretsa masautso pa anthu awa.  
Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.  
Iwowa sanamvere mawu anga  
ndipo anakana lamulo langa.   
 20 Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,  
kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?  
Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;  
nsembe zanu sizindikondweretsa.”   
 21 Choncho Yehova akuti,  
“Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.  
Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;  
anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”   
 22 Yehova akunena kuti,  
“Taonani, gulu lankhondo likubwera  
kuchokera kumpoto;  
mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka  
kuchokera kumathero a dziko lapansi.   
 23 Atenga mauta ndi mikondo;  
ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.  
Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.  
Akwera pa akavalo awo  
ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo,  
kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”   
 24 A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,  
ndipo manja anthu alefukiratu.  
Nkhawa yatigwira,  
ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.   
 25 Musapite ku minda  
kapena kuyenda mʼmisewu,  
pakuti mdani ali ndi lupanga,  
ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.   
 26 Inu anthu anga, valani ziguduli  
ndipo gubudukani pa phulusa;  
lirani mwamphamvu  
ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,  
pakuti mwadzidzidzi wowonongayo  
adzabwera kudzatipha.   
 27 “Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo.  
Uwayese anthu anga  
monga ungayesere chitsulo  
kuti uwone makhalidwe awo.   
 28 Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira  
ndipo akunka nanena zamiseche.  
Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.  
Onse amangochita zoyipa zokhazokha.   
 29 Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;  
mtovu watha kusungunuka ndi moto.  
Koma ntchito yosungunulayo sikupindula  
chifukwa zoyipa sizikuchokapo.   
 30 Iwo ali ngati siliva wotayidwa,  
chifukwa Yehova wawakana.”