9
1 Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi,
ndi maso anga ngati kasupe wa misozi!
Ndikanalira usana ndi usiku
kulirira anthu anga amene aphedwa.
2 Ndani adzandipatsa malo
ogona mʼchipululu
kuti ndiwasiye anthu anga
ndi kuwachokera kupita kutali;
pakuti onse ndi achigololo,
ndiponso gulu la anthu onyenga.
3 “Amapinda lilime lawo ngati uta.
Mʼdzikomo mwadzaza
ndi mabodza okhaokha
osati zoonadi.
Amapitirirabe kuchita zoyipa;
ndipo sandidziwa Ine.”
Akutero Yehova.
4 “Aliyense achenjere ndi abwenzi ake;
asadalire ngakhale abale ake.
Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu.
Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
5 Aliyense amamunamiza mʼbale wake
ndipo palibe amene amayankhula choonadi.
Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza;
amalimbika kuchita machimo.
6 Iwe wakhalira mʼchinyengo
ndipo ukukana kundidziwa Ine,”
akutero Yehova.
7 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa.
Kodi ndingachite nawonso
bwanji chifukwa cha machimo awo?
8 Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa;
limayankhula zachinyengo.
Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake,
koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
9 Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
akutero Yehova.
‘Kodi ndisawulipsire
mtundu wotere wa anthu?’ ”
10 Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri
ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu.
Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako,
ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe.
Mbalame zamlengalenga zathawa
ndipo nyama zakuthengo zachokako.
11 Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja,
malo okhalamo ankhandwe;
ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda
kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”
12 Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”
13 Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala. 14 Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.” 15 Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu. 16 Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”
17 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere;
itanani akazi odziwa kulira bwino.”
18 Anthu akuti, “Abwere mofulumira
kuti adzatilire
mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi
ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.
19 Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti,
‘Aa! Ife tawonongeka!
Tachita manyazi kwambiri!
Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu
chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ”
20 Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova;
tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova.
Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni;
aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
21 Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu
ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa;
yapha ana athu mʼmisewu,
ndi achinyamata athu mʼmabwalo.
22 Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti,
“ ‘Mitembo ya anthu
idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda,
ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola,
popanda munthu woyitola.’ ”
23 Yehova akuti,
“Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake,
kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake,
kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,
24 koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi:
kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa,
kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo,
chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi.
Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,”
akutero Yehova.
25 “Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe. 26 Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”