24
1 “Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze?
Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa?
2 Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo;
amadyetsa ziweto zimene aba.
3 Amalanda abulu a ana amasiye
ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole.
4 Amachotsa mʼmisewu anthu osauka,
ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko.
5 Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu,
amayendayenda kufuna chakudya;
dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo.
6 Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake,
ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa.
7 Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala;
pa nthawi yozizira amasowa chofunda.
8 Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri
ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo.
9 Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere;
ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole.
10 Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala;
amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala.
11 Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa;
amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu.
12 Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda,
anthu ovulala akulirira chithandizo.
Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense.
13 “Pali ena amene amakana kuwala,
amene safuna kuyenda mʼkuwalako
kapena kukhala mʼnjira zake.
14 Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka
ndipo amakapha osauka ndi amphawi;
nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.
15 Munthu wachigololo amadikira chisisira;
iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’
ndipo amaphimba nkhope yake.
16 Mbala zimathyola nyumba usiku,
koma masana zimadzitsekera;
izo zimathawa kuwala.
17 Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera.
Iwo amachita ubale ndi zoopsa za mdima.
18 “Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi;
minda yawo ndi yotembereredwa pa dzikolo
kotero kuti palibe amene amapita ku minda ya mpesa.
19 Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana
ndi momwemonso mmene manda amachotsera omwe achimwa.
20 Mayi wowabereka amawayiwala,
mphutsi zimasangalala powadya;
anthu oyipa sakumbukiridwanso
koma amathyoka ngati mtengo.
21 Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana,
ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye.
22 Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake;
ngakhale munthuyo atakhazikika, alibe chiyembekezo cha moyo wake.
23 Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka,
koma amakhala akupenyetsetsa njira zawo.
24 Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso;
amatsitsidwa ndipo amachotsedwa monga ena onse;
amadulidwa ngati ngala za tirigu.
25 “Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza
ndi kusandutsa mawu anga kukhala wopanda pake?”