2
Nsembe Zachakudya
“ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani, ndipo apite nawo kwa ansembe, ana a Aaroni. Atapeko modzazitsa dzanja ufa wosalala uja kuti ukhale wachikumbutso pamodzi ndi mafuta ndi lubani ndipo atenthe zonsezi pa guwa lansembe kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa chopereka chonse. Iyi ndi nsembe yotentha pa moto ndiponso fungo lokomera Yehova. Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
“ ‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta. Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophika pa chitsulo chamoto, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta. Umuduledule bulediyo ndi kumupaka mafuta; imeneyo ndi nsembe yachakudya. Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophikidwa pa chiwaya, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Munthu azibwera ndi nsembe za chakudya zimene wapanga ndi zinthu zimenezi. Atachipereka kwa wansembe, iyeyu adzipita nacho ku guwa. Wansembeyo atengeko gawo lina la nsembeyo kukhala ufa wachikumbutso kuti ilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse ndipo ayitenthe pa moto monga nsembe yopsereza ya fungo lokomera Yehova. 10 Zotsala za nsembe ya chakudyayo zikhale za Aaroni ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
11 “ ‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi. 12 Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova. 13 Zopereka zako zonse zachakudya uzithire mchere. Usayiwale kuthira mchere pa chopereka chako popeza mcherewo ukusonyeza pangano pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Tsono uzinthira mchere pa chopereka chako chilichonse.
14 “ ‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha. 15 Uchithire mafuta ndi lubani pakuti ndi chopereka cha chakudya. 16 Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova.