UTHENGA WABWINO WA YESU KHRISTU WOLEMBEDWA NDI
LUKA
1
Mawu Oyamba
Ambiri anayesa kufotokoza nkhani ya zimene zinakwaniritsidwa pakati pathu, monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu. Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo, kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa.
Aneneratu za Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi
Mʼmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe dzina lake Zakariya wa gulu la ansembe la Abiya; mkazi wake Elizabeti analinso wa fuko la Aaroni. Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse. Koma analibe ana chifukwa Elizabeti anali wosabereka; ndipo onse anali okalamba.
Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu, Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani. 10 Ndipo nthawi yofukiza lubani itafika, gulu lonse lopembedza linkapemphera kunja.
11 Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira. 12 Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha. 13 Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane. 14 Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake, 15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa. 16 Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. 17 Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.”
18 Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.”
19 Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu. 20 Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”
21 Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu. 22 Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula.
23 Nthawi yake yotumikira itatha, anabwerera kwawo. 24 Zitatha izi, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati ndipo anadzibisa kwa miyezi isanu. 25 Iye anati, “Ambuye wandichitira izi, kuti mʼmasiku ano wandionetsera kukoma mtima kwake ndi kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.”
Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu
26 Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, 27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. 28 Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”
29 Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. 30 Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. 31 Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. 32 Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, 33 ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”
34 Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?”
35 Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. 37 Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”
38 Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”
Mariya Acheza kwa Elizabeti
39 Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya, 40 kumene anakalowa mʼnyumba ya Zakariya nalonjera Elizabeti. 41 Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. 42 Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke! 43 Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine? 44 Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe. 45 Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!”
Nyimbo ya Mariya
46 Ndipo Mariya anati:
“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47 Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49 pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
monga ananena kwa makolo athu.”
56 Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu ndipo kenaka anabwerera kwawo.
Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi
57 Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna. 58 Anansi ndi abale ake anamva kuti Ambuye anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anakondwera naye pamodzi.
59 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya, 60 koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.”
61 Iwo anati kwa iye, “Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli.”
62 Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo. 63 Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” 64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu. 65 Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi. 66 Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye.
Nyimbo ya Zakariya
67 Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti,
68 “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli
chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.
69 Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife
mu nyumba ya mtumiki wake Davide.
70 (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera),
71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu
ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,
72 kuonetsa chifundo kwa makolo athu
ndi kukumbukira pangano lake loyera,
73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:
74 kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu,
ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,
75 mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.
 
76 “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba;
pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,
77 kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso
kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,
78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu,
ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,
79 kuwalira iwo okhala mu mdima
ndi mu mthunzi wa imfa,
kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.”
80 Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli.