22
Yudasi Avomera Kumupereka Yesu
Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu. Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo. Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu. Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi.
Paska Womaliza
Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe. Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati, “Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.”
Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?”
10 Iye anayankha kuti, “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe, 11 ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’ 12 Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.”
13 Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska.
Za Mgonero wa Ambuye
14 Ora litakwana, Yesu ndi ophunzira ake anakhala pa tebulo. 15 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Ine ndakhala ndikuyembekezera kudya Paska uyu ndi inu ndisanamve zowawa. 16 Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”
17 Atanyamula chikho, Iye anayamika ndipo anati, “Tengani ndipo patsiranani pakati panu. 18 Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.”
19 Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”
20 Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu. 21 Koma dzanja la amene akundipereka Ine lili pamodzi ndi langa pa chakudya pano. 22 Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.” 23 Iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndi ndani wa iwo amene akanachita ichi.
Mkangano Pakati pa Ophunzira
24 Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu. 25 Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’ 26 Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira. 27 Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani. 28 Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero. 29 Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine, 30 kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”
Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
31 “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu. 32 Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”
33 Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”
34 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.”
35 Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?”
Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.”
36 Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula. 37 Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”
38 Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.”
Iye anayankha kuti, “Amenewa akwanira.”
Yesu Apemphera ku Phiri la Olivi
39 Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye. 40 Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.” 41 Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti, 42 “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.” 43 Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa. 44 Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi.
45 Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni. 46 Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”
Amugwira Yesu
47 Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone. 48 Koma Yesu anamufunsa kuti, “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?”
49 Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?” 50 Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja.
51 Koma Yesu anayankha kuti, “Zisachitikenso zimenezi!” Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa.
52 Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga? 53 Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”
Petro Akana Yesu
54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali. 55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi. 56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”
57 Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.”
58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.”
Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.”
59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.”
60 Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira. 61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.” 62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.
Asilikali Amuchita Chipongwe Yesu
63 Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya. 64 Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?” 65 Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri.
Yesu Pamaso pa Pilato ndi Herode
66 Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo. 67 Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.”
Yesu anayankha kuti, “Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire. 68 Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe. 69 Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”
70 Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?”
Iye anayankha kuti, “Mwanena ndinu kuti Ndine.”
71 Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.”