24
Yesu Auka kwa Akufa
Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda. Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ” Ndipo anakumbukira mawu ake.
Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse. 10 Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi. 11 Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru. 12 Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo.
Zochitika pa Njira ya ku Emau
13 Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu. 14 Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo. 15 Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi; 16 koma iwo sanamuzindikire.
17 Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?”
Iwo anayima ndi nkhope zakugwa. 18 Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?”
19 Iye anafunsa kuti, “Zinthu zotani?”
Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse. 20 Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye; 21 koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi. 22 Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa 23 koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo. 24 Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.”
25 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena! 26 Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?” 27 Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.
28 Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira. 29 Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo.
30 Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira. 31 Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo. 32 Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?”
33 Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi 34 ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.” 35 Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira
36 Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.”
37 Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa. 38 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu? 39 Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”
40 Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. 41 Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” 42 Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika. 43 Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona.
44 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”
45 Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba. 46 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu. 47 Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu. 48 Inu ndinu mboni za zimenezi. 49 Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.”
Kupita Kumwamba
50 Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa. 51 Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba. 52 Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. 53 Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.