12
Fanizo la Alimi
Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha.
“Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’
“Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa.
“Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena. 10 Kodi simunawerenge lemba lakuti:
“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
wakhala mwala wa pa ngodya.
11 Ambuye achita zimenezi,
ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ”
12 Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita.
Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara
13 Pambuyo pake anatuma ena a Afarisi ndi Aherode kwa Yesu kuti adzamukole mawu ake. 14 Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?”
Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” 16 Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?”
Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”
17 Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
Ndipo anazizwa naye.
Za Ukwati ndi Kuuka kwa Akufa
18 Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. 19 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 20 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. 22 Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. 23 Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?”
24 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? 25 Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 26 Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ 27 Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”
Lamulo Lalikulu Koposa
28 Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?”
29 Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi! 30 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ 31 Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.”
32 Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. 33 Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”
34 Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.
Khristu ndi Mwana wa Yani?
35 Yesu akuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amanena kuti, ‘Khristu ndi Mwana wa Davide?’ 36 Pajatu Davide mwini wake, poyankhula mwa Mzimu Woyera, ananena kuti,
“Ambuye anati kwa Ambuye anga:
‘Khalani pa dzanja langa lamanja
kufikira nditayika adani anu
pansi pa mapazi anu.’
37 Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?”
Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo.
Yesu Achenjeza Anthu za Aphunzitsi a Malamulo
38 Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika. 39 Ndipo amakhala pa mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malo aulemu pa maphwando. 40 Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”
Chopereka cha Mayi Wamasiye
41 Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. 42 Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama.
43 Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. 44 Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”