15
Zopereka Zapadera
Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo, ndipo mukamadzapereka kwa Yehova, nsembe yotentha pa moto ya ngʼombe kapena nkhosa monga fungo lokoma kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena nsembe zina, nsembe yapadera chifukwa cha lumbiro kapena nsembe yoperekedwa mwaufulu kapenanso yoperekedwa pa chikondwerero, munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi. Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ”
“Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka, ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova.
“ ‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova, pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri. 10 Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 11 Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere. 12 Ngakhale zingachuluke chotani, chitani izi kwa iliyonse ya nyamazo.
13 “ ‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova. 14 Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira. 15 Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. 16 Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’ ”
17 Yehova anawuza Mose kuti, 18 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko 19 ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka. 20 Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu. 21 Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka.
Chopereka Chopepesera Machimo Ochita Mosadziwa
22 “ ‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose, 23 lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo, 24 ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa. 25 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo. 26 Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa.
27 “ ‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. 28 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa. 29 Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo.
30 “ ‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake. 31 Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’ ”
Wosasunga Sabata Aphedwa
32 Aisraeli ali mʼchipululu, munthu wina anapezeka akutola nkhuni tsiku la Sabata. 33 Amene anamupeza akutola nkhunizo anabwera naye kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa gulu lonse 34 ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye. 35 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.” 36 Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose.
Mphonje pa Zovala
37 Yehova anawuza Mose kuti, 38 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira. 39 Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu. 40 Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu. 41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”