28
Zopereka za Tsiku ndi Tsiku
1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Lamula Aisraeli kuti, ‘Onetsetsani kuti mukupereka kwa Ine pa nthawi yoyikika, chopereka cha chakudya chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Ine.’ 3 Awuze kuti, ‘Nsembe ya chakudya imene muzipereka pa moto kwa Yehova tsiku ndi tsiku ndi iyi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri, wopanda chilema. 4 Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. 5 Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi. 6 Iyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku imene analamula pa phiri la Sinai kuti ikhale fungo lokoma, nsembe yopsereza pa moto yopereka kwa Yehova. 7 Chopereka chachakumwa chikhale lita imodzi yachakumwa chaukali pa nkhosa iliyonse. Muzithira pamalo opatulika, kupereka kwa Yehova. 8 Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’ ”
Zopereka za pa Sabata
9 “ ‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. 10 Iyi ndi nsembe yopsereza ya pa Sabata iliyonse, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake chachakumwa.’ ”
Zopereka za pa Mwezi
11 “Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema. 12 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; 13 ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova. 14 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka. 15 Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo.
Paska
16 “ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova. 17 Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. 18 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. 19 Koma muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri aamuna a chaka chimodzi, onsewo wopanda chilema. 20 Pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; makilogalamu awiri pa nkhosa yayimuna iliyonse. 21 Kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa asanu ndi awiri aja. 22 Muziphatikizapo mbuzi yayimuna monga nsembe yopepesera machimo anu. 23 Muzikonza zimenezi nthawi zonse, powonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa. 24 Motere muzikonza chakudya cha nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pa masiku asanu ndi awiri ngati fungo lokomera Yehova. Zimenezi ziziperekedwa kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse pamodzi ndi nsembe yachakumwa. 25 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
Madyerero a Masabata
26 “ ‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. 27 Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova. 28 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pazikhala chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri. 29 Ndipo pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja, kilogalamu imodzi. 30 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu. 31 Muzipereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za zakumwa ndi nsembe yake ya chakudya. Onetsetsani kuti nyamazo zilibe chilema.