Obadiya
1
Masomphenya a Obadiya
Masomphenya a Obadiya.
 
Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti,
Tamva uthenga wochokera kwa Yehova:
Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti,
“Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.”
 
“Taona, ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina;
udzanyozedwa kwambiri.
Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,
iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe
ndipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali,
iwe amene umanena mu mtima mwako kuti,
‘Ndani anganditsitse pansi?’
Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhanga
ndi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi,
ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”
akutero Yehova.
“Anthu akuba akanabwera kwa iwe,
kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku,
aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe!
Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
Ngati anthu othyola mphesa akanafika,
kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
Koma Esau adzalandidwa zinthu zonse,
chuma chake chobisika chidzabedwa!
Anthu onse ogwirizana nawo adzakupirikitsira kumalire;
abwenzi ako adzakunyenga ndi kukugonjetsa;
amene amadya chakudya chako adzakutchera msampha,
koma iwe sudzazindikira zimenezi.”
 
Yehova akunena kuti, “Tsiku limenelo,
kodi sindidzawononga anthu onse anzeru a ku Edomu,
anthu odziwa zinthu mʼmapiri a Esau?
Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha,
ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esau
adzaphedwa pa nkhondo.
10 Chifukwa cha nkhanza zimene unachitira mʼbale wako Yakobo,
udzakhala wamanyazi;
adzakuwononga mpaka muyaya.
11 Pamene adani
ankamulanda chuma chake
pamene alendo analowa pa zipata zake
ndi kuchita maere pa Yerusalemu,
pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo.
12 Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wako
pa nthawi ya tsoka lake,
kapena kunyogodola Ayuda
chifukwa cha chiwonongeko chawo,
kapena kuwaseka pa nthawi ya
mavuto awo.
13 Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu anga
pa nthawi ya masautso awo,
kapena kuwanyogodola
pa tsiku la tsoka lawo,
kapena kulanda chuma chawo
pa nthawi ya masautso awo.
14 Sunayenera kudikirira pamphambano ya misewu
kuti uphe Ayuda othawa,
kapena kuwapereka kwa adani awo Ayuda opulumuka
pa nthawi ya mavuto awo.”
 
15 “Tsiku la Yehova layandikira
limene adzaweruza mitundu yonse ya anthu.
Adzakuchitira zomwe unawachitira ena;
zochita zako zidzakubwerera wekha.
16 Iwe unamwa pa phiri langa loyera,
koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza;
iwo adzamwa ndi kudzandira
ndipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi.
17 Koma pa Phiri la Ziyoni padzakhala chipulumutso;
phirilo lidzakhala lopatulika,
ndipo nyumba ya Yakobo
idzalandira cholowa chake.
18 Nyumba ya Yakobo idzasanduka moto
ndipo nyumba ya Yosefe idzasanduka lawi la moto;
nyumba ya Esau idzasanduka chiputu,
ndipo adzayitenthe pa moto ndi kuyipsereza.
Sipadzakhala anthu opulumuka
kuchokera mʼnyumba ya Esau.”
Yehova wayankhula.
 
19 Anthu ochokera ku Negevi adzakhala
ku mapiri a Esau,
ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiri
adzatenga dziko la Afilisti.
Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya,
ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi.
20 Aisraeli amene ali ku ukapolo
adzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati;
a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradi
adzalandira mizinda ya ku Negevi.
21 Opulumukawo adzapita ku Phiri la Ziyoni
ndipo adzalamulira mapiri a Esau.
Koma ufumuwo udzakhala wa Yehova.