4
Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Ndinu chimwemwe changa ndi chipewa cha ulemerero wanga. Abwenzi okondedwa, chilimikani choncho mwa Ambuye.
Ndikudandaulira Euodiya ndi Suntuke kuti akhale ndi mtima umodzi mwa Ambuye. Inde, ndikupempha iwe mnzanga pa ntchitoyi, thandiza amayiwa amene ndagwira nawo ntchito ya Uthenga Wabwino pamodzi ndi Klementonso ndi ena onse antchito anzanga amene mayina awo ali mʼbuku lamoyo.
Malangizo Otsiriza
Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa! Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi. Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka. Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.
Kuthokoza Chifukwa cha Mphatso
10 Ndikukondwa kwambiri mwa Ambuye kuti patapita nthawi tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizira. Zoonadi, mwakhala mukundikumbukira, koma munalibe mpata woti muonetsere zimenezi. 11 Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. 12 Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. 13 Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.
14 Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. 15 Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu. 16 Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga. 17 Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. 18 Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. 19 Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.
20 Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni.
Malonje Otsiriza
21 Perekani moni kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akupereka moni wawo. 22 Oyera mtima onse akupereka moni, makamaka iwo a ku nyumba ya Kaisara.
23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Ameni.