2
Ubwino Wanzeru
Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga
ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,
ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru
ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;
ngati upempha kuti uzindikire zinthu
inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,
ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva
ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,
ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova;
ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru,
ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo.
Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama.
Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.
 
Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo,
kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
10 Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako,
kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.
11 Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga;
kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.
 
12 Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa,
kwa anthu amabodza,
13 amene amasiya njira zolungama
namayenda mʼnjira zamdima,
14 amene amakondwera pochita zoyipa
namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.
15 Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota,
ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.
 
16 Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo;
kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,
17 amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake
ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.
18 Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa;
njira zake zimamufikitsa ku manda.
19 Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera
kapena kupezanso njira zamoyo.
 
20 Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino,
uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.
21 Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko
ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;
22 Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo,
ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.