12
Mayi ndi Chinjoka
Chizindikiro chachikulu chinaoneka kuthambo; mayi atavala dzuwa, mapazi ake ataponda mwezi, pamutu pake pali chipewa chaufumu chokhala ndi nyenyezi khumi ndi ziwiri. Mayiyo anali woyembekezera ndipo pa nthawi yake yochira analira mokuwa chifukwa cha ululu wakubala. Kenaka ku thambo kunaonekanso chizindikiro china; chinjoka chachikulu kwambiri, chofiira chomwe chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi; pamutu uliwonse chitavala chipewa chaufumu. Mchira wake unakokolola gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi kuzichotsa ku thambo ndi kuziponya pa dziko lapansi. Chinjoka chija chinadzayima patsogolo pa mayi uja amene anali pafupi kuberekayu kuti mwanayo akangobadwa chimudye. Mayiyo anabereka mwana wamwamuna amene adzalamulira anthu a mitundu ina yonse ndi ndodo yachitsulo. Ndipo mwanayo analandidwa ku dzanja la mayiyo ndi kupita naye kwa Mulungu ku mpando wake waufumu. Mayiyo anathawira ku chipululu ku malo kumene Mulungu anamukonzera, kumene akasamalidweko masiku 1,260.
Zitatero, kumwamba kunayambika nkhondo. Mikayeli ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho ndi angelo ake anabwezeranso. Koma analibe mphamvu ndipo anagonjetsedwa nathamangitsidwa kumwambako. Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.
10 Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti,
“Tsopano chipulumutso, mphamvu,
ufumu wa Mulungu wathu
ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera.
Pakuti woneneza abale athu uja,
amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku,
wagwetsedwa pansi.
11 Abale athuwo anamugonjetsa
ndi magazi a Mwana Wankhosa
ndiponso mawu a umboni wawo.
Iwo anadzipereka kwathunthu,
moti sanakonde miyoyo yawo.
12 Choncho, kondwerani, inu dziko lakumwamba
ndi onse okhala kumeneko!
Koma tsoka dziko lapansi ndi nyanja
chifukwa Mdierekezi wagwetsedwa kwa inu!
Iye wadzazidwa ndi ukali
chifukwa akudziwa kuti nthawi yake ndi yochepa.”
13 Pamene chinjokacho chinaona kuti chagwetsedwa pa dziko lapansi, chinayamba kuthamangitsa mayi uja amene anali atabala mwana wamwamunayu. 14 Mayiyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athawire ku malo ake aja a ku chipululu. Kumeneko adzasamalidwako zaka zitatu ndi theka kuti chinjoka chija chisamupeze. 15 Kenaka chinjoka chija chinalavulira mayiyo madzi ambiri ngati mtsinje, kuti madziwo amukokolole. 16 Koma dziko lapansi linamuthandiza mayiyo. Nthaka inatsekuka ndi kumeza mtsinje uja unachokera mʼkamwa mwa chinjokacho. 17 Pamenepo chinjokacho chinamupsera mtima mayiyo ndipo chinachoka kupita kukachita nkhondo ndi ana ena onse a mayiyo, ndiye kuti anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.
18 Kenaka ndinaona chinjokacho chitayima mʼmbali mwa nyanja.