8
Yehova Alonjeza Kudalitsa Yerusalemu
1 Awa ndi mawu amene Yehova Wamphamvuzonse ananena. 2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikuchitira nsanje yayikulu Ziyoni. Mtima wanga ukupweteka chifukwa cha nsanje pa iyeyo.”
3 Yehova akuti, “Ndidzabwerera ku Ziyoni ndi kukakhala ku Yerusalemu. Pamenepo Yerusalemu adzatchedwa Mzinda wa Choonadi ndipo phiri la Yehova Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Lopatulika.”
4 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Abambo ndi amayi okalamba adzakhalanso mʼmisewu ya mu Yerusalemu, aliyense ali ndi ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha kuchuluka kwa masiku ake. 5 Ndipo misewu ya mu mzindamo idzadzaza ndi anyamata ndi atsikana akusewera.”
6 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
7 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani ndidzapulumutsa anthu anga kuchokera ku mayiko a kummawa ndi kumadzulo. 8 Ndidzawabweretsa kuti adzakhale mu Yerusalemu; adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, wokhulupirika ndi wolungama pakati pawo.”
9 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Inu amene tsopano mukumva mawu awa amene akuyankhula aneneri amene analipo pamene ankayika maziko a nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, ‘limbani mtima kuti mumange Nyumba ya Yehova.’ 10 Mpaka nthawi imeneyi panalibe munthu wolandira malipiro pa ntchito kapena ndalama zolipirira nyama zogwira ntchito. Panalibe munthu amene ankadzigwirira ntchito mwamtendere chifukwa choopa adani ake, pakuti Ine ndinkawayambanitsa. 11 Koma tsopano sindidzachitira otsala mwa anthu awa zomwe ndinachita kale,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
12 “Pakuti mbewu zidzamera bwino, mpesa udzabala zipatso zake, nthaka idzatulutsa zomera zake, ndi thambo lidzagwetsa mame. Ndidzapereka zonse kukhala cholowa cha otsala mwa anthu awa. 13 Monga mwakhala muli chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu ina ya anthu, inu Yuda ndi Israeli, choncho ndidzakupulumutsani, ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha, koma limbani mtima.”
14 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Monga ndinatsimikiza mtima kubweretsa choyipa pa inu, komanso osakuchitirani chisoni pamene makolo anu anandikwiyitsa,” akutero Yehova, 15 “Choncho tsopano ndatsimikiza mtima kuchitiranso zabwino Yerusalemu ndi Yuda. Musachite mantha. 16 Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu; 17 musamachitire mnzanu chiwembu, musamakonde kulumbira zonama. Zonsezi Ine ndimadana nazo,” akutero Yehova.
18 Yehova Wamphamvuzonse anayankhulanso nane. 19 Ndipo ananena kuti, “Kusala zakudya kwa pa mwezi wachinayi, chisanu, chisanu ndi chiwiri ndi wakhumi, kudzakhala nthawi yachimwemwe, ya chisangalalo ndi nthawi ya madyerero chikondwerero kwa Yuda. Nʼchifukwa chake muzikonda choonadi ndi mtendere.”
20 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a mitundu yambiri ndi anthu okhala mʼmizinda yambiri adzabwerabe, 21 ndipo nzika za mzinda wina zidzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe madalitso kwa Yehova ndi kukapembedza Yehova Wamphamvuzonse. Inenso ndikupita kumeneko.’ 22 Anthu ambiri ndiponso a ku mayiko amphamvu adzabwera ku Yerusalemu kudzapembedza Yehova Wamphamvuzonse ndi kudzapempha madalitso.”
23 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”