14
Yehova Akubwera ndipo Akulamulira
1 Taonani tsiku la Yehova likubwera pamene zinthu zimene adani ako anakulanda azidzagawana iwe ukuona.
2 Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu; mzindawu udzalandidwa, nyumba zidzaphwasulidwa, ndipo akazi adzagwiriridwa. Theka la anthu a mu mzindamu lidzapita ku ukapolo, koma ena onse otsala mu mzindamu sadzachotsedwa.
3 Pamenepo Yehova adzabwera kudzamenyana ndi mitundu ya anthu imeneyi, ngati mmene amachitira pa nthawi ya nkhondo. 4 Tsiku limenelo adzayimirira pa Phiri la Olivi, kummawa kwa Yerusalemu, ndipo Phiri la Olivilo lidzagawikana pawiri kuyambira kummawa mpaka kumadzulo, kupanga chigwa chachikulu, kuchititsa kuti theka la phiri lisunthire kumpoto ndi linalo kummwera. 5 Inu mudzathawa podzera mʼchigwa chapakati pa phirilo, pakuti chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa monga munachitira pa tsiku la chivomerezi nthawi ya Uziya mfumu ya Yuda. Kenaka Yehova Mulungu wanga adzabwera, pamodzi ndi oyera ake onse.
6 Tsiku limenelo sipadzakhala kuwala, kuzizira kapena chisanu. 7 Lidzakhala tsiku lapaderadera, silidzakhala usana kapena usiku; tsiku limeneli akulidziwa ndi Yehova yekha. Ikadzafika nthawi ya madzulo, kudzakhala kukuwalabe.
8 Tsiku limenelo madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu, theka lidzapita ku nyanja ya kummawa ndipo theka lina ku nyanja ya kumadzulo, nthawi yachilimwe ndi nthawi yozizira yomwe.
9 Ndipo Yehova adzakhala mfumu pa dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo padzakhala Ambuye mmodzi yekha, ndipo dzina lidzakhala limodzi lomwelo.
10 Dziko lonse, kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kummwera kwa Yerusalemu, lidzakhala ngati Araba. Koma Yerusalemu adzakwezedwa ndipo adzakhala pamalo pakepo, kuyambira ku Chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene ali ku Chipata Choyamba, ku Chipata Chapangodya, ndipo kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku malo opsinyira mphesa za mfumu. 11 Mʼmenemo mudzakhala anthu; sadzawonongedwanso. Yerusalemu adzakhala pa mtendere.
12 Mliri umene Yehova adzakanthire nawo mitundu yonse ya anthu imene inkamenyana ndi Yerusalemu ndi uwu: Matupi awo adzawola iwo eni akuyenda, maso awo adzawola ali mʼmalo mwake, ndipo malilime awo adzawola ali mʼkamwa mwawo. 13 Pa tsiku limenelo Yehova adzasokoneza anthu akuluakulu. Munthu aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndi kuyamba kumenyana okhaokha. 14 Yuda nayenso adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Chuma chonse cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi; golide, siliva ndi zovala zochuluka kwambiri. 15 Mliri womwewo udzapha akavalo ndi nyulu, ngamira ndi abulu, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku misasako.
16 Kenaka opulumuka ochokera mwa mitundu yonse ya anthu amene anathira nkhondo Yerusalemu, azidzapita chaka ndi chaka kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, ndiponso kukachita Chikondwerero cha Misasa. 17 Ngati mitundu ina ya anthu pa dziko lapansi sidzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, idzakhala wopanda mvula. 18 Ndipo ngati anthu a ku Igupto sadzapita ndi kukakhala nawo kumeneko, adzakhala wopanda mvula. Yehova adzabweretsa pa iwo mliri umene analangira mitundu ina ya anthu imene sinapite ku Chikondwerero cha Misasa. 19 Chimenechi chidzakhala chilango cha Igupto ndiponso mitundu ina yonse imene sidzapita ku Chikondwerero cha Misasa.
20 Pa tsiku limenelo pa maberu a akavalo padzalembedwa mawu oti wopatulikira Yehova, ndipo miphika ya mʼNyumba ya Yehova idzakhala yopatulika ngati mbale za ku guwa. 21 Mʼphika uliwonse ku Yerusalemu ndi ku Yuda udzakhala wopatulikira Yehova Wamphamvuzonse, ndipo onse amene adzabwera kudzapereka nsembe adzatenga miphika ina ndi kuphikiramo. Ndipo nthawi imeneyo simudzakhalanso Akanaani mʼNyumba ya Yehova Wamphamvuzonse.