10
Paulo Ateteza Utumiki Wake
Mwa kufatsa ndi kuleza mtima kwa Khristu, ndikukupemphani, ine Paulo amene anthu ena amati ndimachita manyazi tikaonana maso ndi maso ndi inu, koma wosaopa pamene ndili kutali nanu! Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kumeneko ndisadzachite kuyankhula mwamphamvu monga mmene ndimayembekezera kudzachita kwa anthu ena amene amaganiza kuti machitidwe athu ndi ofanana ndi anthu a dziko lapansi. Ngakhale ife timakhala mʼdziko lapansi, sitimenya nkhondo monga mmene dziko lapansi limachitira. Pakuti zida zathu zankhondo si zida za dziko lapansi. Koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kugwetsa malinga. Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu. Ndipo ife tidzakhala okonzeka kulanga aliyense wosamvera ngati inuyo mutakhala omvera kwenikweni.
Inu mukuweruza potengera zimene maso anu akuona. Ngati wina akutsimikiza kuti ndi wake wa Khristu, iye aganizenso kuti ifenso ndife a Khristu monga iye. Tsono ngakhale nditadzitama momasuka za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa woti tikukuzeni osati kukuwonongani, ndithu sindidzachita manyazi. Ine sindikufuna kuoneka ngati ndikukuopsezani ndi makalata anga. 10 Pakuti ena amati, “Makalata ake ndi awukali ndi amphamvu koma maonekedwe a thupi lake ndi wosagwira mtima ndipo mayankhulidwe ake ndi achabechabe.” 11 Anthu oterewa ayenera kuzindikira kuti zomwe timalemba mʼmakalata tili kutali ndi zomwe tidzakhale tili komweko.
12 Sitikudziyika kapena kudzifananiza tokha ndi anthu ena amene amadziyenereza okha. Pamene akudzifanizira okha podziyerekeza ndi anzawo a mʼgulu lawo lomwe, ndi opanda nzeru. 13 Komabe, ifeyo sitidzitama modutsa malire ake enieni, koma kudzitama kwathu kudzalekeza mʼmalire amene Mulungu anatiyikira, malire ake ndi mpaka kwa inu. 14 Pakuti sitikudzitama modutsa malire ngati kuti sitinafike kwa inu, popeza tinali oyamba kufika kwa inu ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. 15 Choncho sitinyadiranso ntchito imene ena anayigwira. Chiyembekezo chathu nʼchakuti, pamene chikhulupiriro chanu chikukulirakulira, dera lathu la ntchito pakati panu lidzakulanso kwambiri, 16 kuti tikalalikire Uthenga Wabwino mu zigawo zina kupitirira kwanuko. Pakuti sitikufuna kudzitama pa ntchito yogwira ena kale mʼdera la munthu wina. 17 Koma, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.” 18 Pakuti munthu amene amavomerezedwa, si amene amadziyenereza yekha, koma munthu amene Ambuye amuyenereza.