21
Nsembe Yopepesera Munthu Akaphedwa Mosadziwika Bwino
1 Ngati munthu apezeka ataphedwa mʼmunda mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kukhala lanu koma inu osadziwa amene wamupha,
2 akuluakulu anu ndi oweruza adzapite ndi kuyeza kutalikirana kuchokera pamene pali mtembowo ndi mizinda yoyandikira.
3 Kenaka akuluakulu a mzinda wapafupi kwambiri ndi mtembowo adzatenge ngʼombe imene sinagwirepo ntchito kapena kuvalapo goli
4 ndi kuyikusira ku chigwa chimene sichinalimidwepo ndiponso kumene kuli mtsinje woyenda. Ku chigwa kumeneko ayenera kukayithyola khosi ngʼombeyo.
5 Ansembe, ana a Aaroni, adzapite patsogolo pangʼono, popeza ndiwo amene Yehova Mulungu wanu anawasankha kuti azitumikira, kupereka mdalitso mʼdzina la Yehova ndi kugamula milandu yonse yamikangano ndi yovulazana.
6 Kenaka akuluakulu a mzinda wapafupi kwambiri ndi mtembowo adzasamba mʼmanja pamwamba pa ngʼombe yothyoledwa khosi ija,
7 nadzatsimikiza kuti, “Manja athu sanakhetse magazi awa ndipo sitinaonerere kuphedwako.
8 Yehova, landirani nsembe yopepesa ya anthu anu Aisraeli amene munawapulumutsa, ndipo muwakhululukire tchimo la kupha munthu wosalakwa.” Mukatero ndiye kuti adzapezeka kuti ndi osalakwa.
9 Kotero mudzadzichotsera nokha tchimo lokhetsa magazi wosalakwa, popeza mwachita zoyenera pamaso pa Yehova.
Kukwatira Mkazi Wogwidwa ku Nkhondo
10 Mukapita kukachita nkhondo ndi adani anu, Yehova Mulungu wanu nawapereka adani anuwo mʼmanja mwanu muwagwira ukapolo,
11 ndiye ngati muona mkazi wokongola pakati pa ogwidwawo nakutengani mtima, mukhoza kumutenga kuti akhale mkazi wanu.
12 Mumutengere ku nyumba kwanu, kumumeta tsitsi lake, mumuwenge zikhadabo zake
13 ndipo avulidwe zovala zimene anagwidwa nazo. Atakhala mʼnyumba mwanu nalira maliro a abambo ndi amayi ake kwa mwezi wathunthu, ndiye mukhoza kupita kwa iye ndi kukhala mwamuna wake ndipo iyeyo adzakhala mkazi wanu.
14 Ngati simukukondweretsedwa naye, muloleni kuti apite kumene afuna. Musamugulitse kapena kumuzunza ngati kapolo, popeza mwamuchotsa ulemu.
Ufulu wa Mwana Woyamba Kubadwa
15 Ngati munthu ali ndi akazi awiri, nakonda wina koposa mnzake, onsewa ndikubereka ana aamuna koma woyamba nakhala mwana wa mkazi amene samukondayo,
16 akamagawa chuma chake akanali moyo kwa ana akewo, asapereke ufulu wa mwana woyamba kubadwa kwa mwana wamwamuna wa mkazi amene amamukonda mʼmalo mwa mwana wake woyamba kubadwa weniweni amene ndi mwana wamkazi amene samukonda.
17 Iye ayenera kuonetsa kuti mwana wake wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa pomupatsa miyeso iwiri ya zonse zimene ali nazo. Mwana wamwamuna ameneyo ndiye chizindikiro cha mphamvu za abambo ake. Ufulu wokhala mwana wamwamuna woyamba ndi wake.
Mwana Wamwamuna Wowukira
18 Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wowukira amene samvera a abambo ake ndi amayi ake akamuweruza,
19 abambo ndi amayi ake amugwire ndi kupita naye kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda wake ndipo
20 akawawuze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu wamwamunayu ndi wosamva ndi wowukira. Iyeyu satimvera. Ndi mwana wadyera komanso ndi chidakwa.”
21 Pamenepo anthu onse a mu mzinda wake adzamuphe ndi miyala. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu. Aisraeli onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha.
Malamulo Osiyanasiyana
22 Ngati munthu wopezeka ndi mlandu wopha mnzake waphedwa ndipo mtembo wake wapachikidwa pamtengo,
23 musasiye mtembowo pa mtengopo usiku wonse. Muonetsetse kuti mwakawukwirira tsiku lomwelo, chifukwa aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu. Musayipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani ngati cholowa chanu.