4
Matsoka ndi Mavuto a Moyo Uno
1 Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano:
ndinaona misozi ya anthu opsinjika,
ndipo iwo alibe owatonthoza;
mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo
ndipo iwonso analibe owatonthoza.
2 Ndipo ndinanena kuti akufa,
amene anafa kale,
ndi osangalala kuposa amoyo,
amene akanalibe ndi moyo.
3 Koma wopambana onsewa
ndi amene sanabadwe,
amene sanaone zoyipa
zimene chimachitika pansi pano.
4 Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
5 Chitsiru chimangoti manja ake lobodo
ndi kudzipha chokha ndi njala.
6 Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere,
kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto,
ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.
7 Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:
8 Panali munthu amene anali yekhayekha;
analibe mwana kapena mʼbale.
Ntchito yake yolemetsa sinkatha,
ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake.
Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani?
Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?”
Izinso ndi zopandapake,
zosasangalatsa!
9 Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,
chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:
10 Ngati winayo agwa,
mnzakeyo adzamudzutsa.
Koma tsoka kwa munthu amene agwa
ndipo alibe wina woti amudzutse!
11 Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana.
Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
12 Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa,
koma anthu awiri akhoza kudziteteza.
Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.
Kutukuka Nʼkopandapake
13 Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.
14 Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo.
15 Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu.
16 Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.