31
Mkungudza mu Lebanoni
1 Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti,
“ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
3 Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,
wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango.
Unali wautali,
msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
4 Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo,
akasupe ozama ankawutalikitsa.
Mitsinje yake inkayenda
mozungulira malo amene unaliwo
ndipo ngalande zake zinkafika
ku mitengo yonse ya mʼmunda.
5 Choncho unatalika kwambiri
kupambana mitengo yonse ya mʼmunda.
Nthambi zake zinachuluka
ndi kutalika kwambiri,
chifukwa inkalandira madzi ambiri.
6 Mbalame zonse zamlengalenga
zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo.
Nyama zakuthengo zonse
zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake.
Mitundu yotchuka ya anthu
inkakhala mu mthunzi wake.
7 Unali wokongola kwambiri,
wa nthambi zake zotambalala,
chifukwa mizu yake inazama pansi
kumene kunali madzi ochuluka.
8 Mʼmunda wa Mulungu munalibe
mkungudza wofanana nawo,
kapena mitengo ya payini
ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake.
Munalibenso mtengo wa mkuyu
nthambi zofanafana ndi zake.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse
wofanana ndi iwo kukongola kwake.
9 Ine ndinawupanga wokongola
wa nthambi zochuluka.
Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa
Mulungu inawuchitira nsanje.
10 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake,
11 ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake.
12 Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya.
13 Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake.
14 Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
15 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma.
16 Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi.
17 Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.
18 “ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo.
“ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”