40
Malo Atsopano a Nyumba ya Mulungu
1 Kumayambiriro a chaka cha 25, cha ukapolo wathu, tsiku la khumi lamwezi, patapita zaka khumi ndi zinayi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, pa tsiku lomwelo dzanja la Yehova linali pa ine ndipo Iye anapita nane ku Yerusalemu.
2 Mʼmasomphenyawo Yehova ananditenga ndi kupita nane ku dziko la Israeli ndipo anandiyika pa phiri lalitali kwambiri, moti ndinaona ngati mzinda.
3 Atandifikitsa kumeneko ndinaona munthu wonyezimira ngati mkuwa. Iye anali atayima pa chipata ndipo mʼdzanja lake munali chingwe cha nsalu yabafuta ndi ndodo yoyezera.
4 Munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetse bwinobwino. Uyikepo mtima wako pa zonse zimene ndikukuonetsa pakuti anakubweretsa kuno kuti uwone zimenezi. Tsono ukawawuze Aisraeli zonse zimene uzione.”
Chipata Chakummawa
5 Ine ndinaona khoma litazungulira mbali zonse za Nyumba ya Mulungu. Mʼdzanja la munthuyo munali bango lopimira limene kutalika kwake kunali kwa mamita atatu. Atayeza chipupacho anapeza kuti kuchindikira kwake kunali mamita atatu, ndiponso kutalika kwake kunalinso mamita atatu.
6 Anapita ku chipata chakummawa. Anakwera pa makwerero a nyumbayo, nayeza chiwundo choyamba cha chipatacho; kutalika kwake kunali mamita atatu.
7 Kudutsa chiwundo choyambachi, panali zipinda za alonda zisanu ndi chimodzi, zitatu kudzanja lamanja, zitatu kudzanja lamanzere. Chilichonse chinali cha mamita atatu mulitali mwake, chimodzimodzinso mulifupi mwake. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita awiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pa chipata pafupi ndi khonde lapachipata, chinali mamita atatu.
8 Ndipo iye anayeza khonde la chipata ndipo chinali cha mamita atatu.
9 Anayeza khonde ndipo linali mamita anayi. Mphuthu zake zinali mita imodzi kuchindikira kwake. Khonde lamʼkati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu.
10 Mʼkati mwa chipata chakummawa munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zofanana, ndipo khonde la pakati pa zipindazo linali lofanana.
11 Kenaka anayeza chipata cholowera; mulifupi mwake munali mamita asanu ndipo mulitali mwake munali mamita asanu ndi limodzi ndi theka.
12 Kutsogolo kwa chipinda chilichonse cha alonda kunali khoma lalifupi lotalika theka la mita, ndipo mbali iliyonse ya zipinda za alondazo inali yotalika mamita atatu.
13 Ndipo anayeza kutalika kwa mulifupi mwa chipata cholowera, kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china; kuchokera ku chitseko mpaka ku chitseko china. Kutalika kwake kunali mamita khumi ndi awiri ndi theka.
14 Anayezanso khonde lamʼkati ndipo linali la mamita makumi atatu. Ndipo mozungulira khondelo munali bwalo. Muyesowu sukuphatikiza khonde loyangʼanana ndi bwalo.
15 Kuchokera pa chipata cholowera mpaka ku mapeto a khonde la chipata, kutalika kwake kunali mamita 27.
16 Makoma a zipinda ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lamʼkati linalinso ndi mazenera mʼkati mwake. Pa makoma onsewo anajambulapo zithunzi za kanjedza.
Bwalo la Kunja
17 Kenaka munthuyo anandilowetsa mʼbwalo lakunja, ndipo ndinaona zipinda zina ndi msewu wa miyala wozungulira bwalo lonse. Zipinda zonse zinali makumi atatu ndipo zinkayangʼana msewuwo.
18 Utali wa mulifupi mwa msewuwo unkayenda mamita 27 kufanana ndi utali wa chipata cholowera. Uwu unali msewu wa mʼmunsi.
19 Tsono, anayeza kutalika kwa bwalo kuyambira chipata cholowera choyamba mpaka polowera pa chipata chakunja cha bwalo la mʼkati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipata Chakumpoto
20 Kenaka munthuyo anayeza mulitali ndi mulifupi mwa chipata chimene chimayangʼana kumpoto, chotulukira kunja.
21 Zipinda za alonda zimene zinalipo zitatu mbali iliyonse, makoma ake ndi khonde zinali ndi muyeso wofanana ndi wachipata choyamba chija. Kutalika kwake kunali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
22 Mipata yake, khonde lake ndi zojambula za kanjedza zinali ndi miyeso yofanana ndi za chipata chakummawa. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndipo kotsirizira kwa chipatacho kunali khonde.
23 Panalinso chipata cholowera ku bwalo lamʼkati chofanana ndi chakummawa chimene chimayangʼanana ndi chipata chakumpoto, chofanana ndi cha mbali ya kummawa. Anachiyeza kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipata Chakummwera
24 Ndipo munthuyo anapita nane ku mbali yakummwera ndipo ndinaona chipata chakummwera. Iye anayeza mphuthu zake ndi khonde ndipo zinali ndi miyeso yofanana ndi ya zina zija.
25 Mʼzipinda za chipata cholowera chimenechi ndi mʼkhonde lake munali mipata yofanana ndi ya mʼzipinda zina. Mulitali mwake munali mamita 27, mulifupi mwake munali mamita 13.
26 Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndi khonde kotsirizira kwake. Chipindacho chinali ndi zojambula za kanjedza ku mbali zonse za makoma.
27 Bwalo lamʼkati linalinso ndi chipata kummwera. Munthuyo analiyeza kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Zipata Zolowera ku Bwalo la Mʼkati
28 Ndipo munthu uja anandilowetsa mʼbwalo lamʼkati kudzera ku chipata chakummwera. Anayeza chipatachi ndipo chinali chofanana ndi zinzake zija.
29 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake zinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi munali mamita 13.
30 (Khonde lililonse la makonde atatu a zipata zolowera bwalo lamʼkati aja linali la mamita ozungulira mʼbwalo lamʼkati anali mamita 13 mulitali mwake, mamita awiri ndi theka mulifupi mwake).
31 Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
32 Kenaka munthuyo anapita nane ku bwalo la mʼkati mbali ya kummawa, ndipo anayeza chipata cholowera; chinali chofanana ndi zinzake zina zija.
33 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake chinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
34 Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
35 Kenaka anapita nane ku chipata chakumpoto ndipo anachiyeza. Chinali chofanana ndi zina zija.
36 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndiponso khonde lake zinali zofanana ndi zina zija, ndipo chinalinso ndi mipata mbali zonse ziwiri. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
37 Khonde lake limayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu zake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
Zipinda Zokonzeramo Nsembe
38 Panali chipinda ndipo khomo lake linali pafupi ndi khonde la chipata cholowera chamʼkati. Mʼchipinda mʼmenemo ankatsukira nyama ya nsembe yopsereza.
39 Pa khonde la chipatacho panali matebulo awiri, lina kuno lina uko. Ankapherapo nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula.
40 Panali matebulo anayi, awiri a iwo anali kunja kwa khoma la khonde pafupi ndi makwerero olowera pa chipata chakumpoto ndi awiri enawo anali mbali inayo ya makwerero.
41 Choncho ku mbali imodzi ya chipata kunali matebulo anayi, ndiponso ku mbali inayo kunali matebulo anayi. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pa matebulopo ankapherapo nyama za nsembe zopsereza.
42 Matebulo anayiwa anali a miyala yosema. Lililonse mulitali mwake linali la masentimita 75, mulifupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita makumi asanu. Pa matebulopo amayikapo zipangizo zophera nsembe zopsereza ndi nsembe zina.
43 Choncho pa matebulopo ankayikapo nyama za nsembe zopsereza. Mbedza zitatu zazitali ngati chikhatho amazikoleka pa makoma pozungulira ponse.
Zipinda za Ansembe
44 Munthu uja anapita nane mʼkati mwa bwalo ndipo ndinaona zipinda ziwiri. Chimodzi chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyangʼana kummwera ndi china chinali pafupi ndi chipata chakummwera kuyangʼana kumpoto.
45 Munthuyo anandiwuza kuti, “Chipinda chimene chikuyangʼana kummwera ndi cha ansembe amene amayangʼanira Nyumba ya Mulungu,
46 ndipo chipinda chimene chikuyangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amayangʼanira guwa lansembe. Amenewa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene ayenera kutumikira pamaso pa Yehova mʼNyumba ya Mulungu.”
47 Kenaka munthuyo anayeza bwalo; linali lofanana mbali zonse kutalika kwake, mulitali mwake munali mamita 53, ndipo mulifupi mwake munali mamita 53. Ndipo guwa lansembe linali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
Nyumba ya Mulungu
48 Munthuyo anapita nane pa khonde la Nyumba ya Mulunguyo. Anayeza mphuthu za khondelo ndipo zinali mamita awiri ndi theka mbali zonse. Mulifupi mwa chipatacho munali mamita asanu ndi awiri ndipo mulifupi mwa makoma ake munali mamita awiri mbali zonse.
49 Mulitali mwa khonde munali mamita khumi, mulifupi mwake munali mamita asanu ndi limodzi kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. Panali makwerero khumi, ndipo mbali zonse kunali nsanamira.