KALATA YA PAULO YOLEMBERA
AEFESO
1
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu.
Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu:
2 Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
Madalitso Auzimu mwa Khristu
3 Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.
4 Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake,
5 Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake.
6 Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda.
7 Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu
8 chimene anatipatsa mosawumira. Mwa nzeru zonse ndi chidziwitso,
9 Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake.
10 Chimene anakonza kuti chichitike nʼchakuti, ikakwana nthawi yake asonkhanitsa pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za kumwamba ndi pa dziko lapansi.
11 Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake,
12 nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake.
13 Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.
14 Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.
Kuyamika ndi Kupemphera
15 Choncho, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse,
16 ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga.
17 Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni.
18 Ndimapempheranso kuti maso a mitima yanu atsekuke ndi cholinga choti mudziwe chiyembekezo chimene Iye anakuyitanirani, chuma cha ulemerero chomwe chili mwa anthu oyera mtima.
19 Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu zake zazikulu koposa zimene zili mwa ife amene timakhulupirira. Mphamvuyi ndi yofanana ndi mphamvu yoposa ija
20 imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba.
21 Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo.
22 Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo,
23 umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse.