2
Mfumu Ikwatira Estere
1 Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza.
2 Tsono anyamata a mfumu amene ankamutumikira anati, “Mfumu, akufunireni anamwali okongola.
3 Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola.
4 Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo.
5 Myuda wina wa fuko la Benjamini, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi, anali mu mzinda wa Susa.
6 Iyeyu anali mmodzi mwa anthu amene anatengedwa ukapolo ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda.
7 Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira.
8 Lamulo la mfumu atalilengeza ndi kubwera nawo pamodzi anamwali ambiri ku mzinda wa Susa kuti akasamalidwe ndi Hegai, Estere nayenso anatengedwa kupita naye ku nyumba ya mfumu kuti akasamalidwe ndi Hegai woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi uja.
9 Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi.
10 Estere sanawulule mtundu wake ndi abale ake chifukwa Mordekai anamuletsa kutero.
11 Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayendayenda pafupi ndi bwalo la nyumba yosungiramo akazi ija kuti adziwe za moyo wa Estere ndi kuti zinthu zikumuyendera bwanji.
12 Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa.
13 Ndipo namwali ankapita kwa mfumu motere: Ankaloledwa kutenga chilichonse angafune mʼnyumba yosungiramo akazi kupita nacho ku nyumba ya mfumu.
14 Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake.
15 Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye.
16 Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.
17 Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.
18 Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu.
Mordekai Awulula Chiwembu
19 Anamwali atasonkhanitsidwa pamodzi, Mordekai anakhala pansi pa chipata cha mfumu.
20 Koma Estere anali asanawululebe za mtundu wake ndi anthu a pa banja lake monga momwe analamulira Mordekai, chifukwa anapitirira kutsata malangizo a Mordekai monga ankachitira pamene ankamulera.
21 Pa nthawi imene Mordekai ankalondera pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa amfumu, olondera pa khomo la nyumba yake, anayipidwa mtima ndipo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero.
22 Koma Mordekai atazindikira za chiwembuchi anawuza mfumukazi Estere ndipo iye anakawuza mfumu mʼmalo mwa Mordekai.
23 Ndipo pamene anafufuza za chiwembuchi kuti zinali zoona, adindo awiriwa anaphedwa monyongedwa. Zinthu izi zinalembedwa mʼbuku la Mbiri ndi kusungidwa ndi Mfumu.