12
Kukhazikitsidwa kwa Paska
1 Yehova anayankhula kwa Mose ndi Aaroni mʼdziko la Igupto kuti,
2 “Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba wa chaka.
3 Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi.
4 Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere.
5 Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi.
6 Muzisunge mpaka tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi, pamene gulu lonse la Aisraeli lidzaphe nyamazo madzulo.
7 Ndipo adzatengeko magazi anyamazo ndi kuwaza pa mphuthu ziwiri za chitseko ndiponso pamwamba pa chitseko cha nyumba mmene adzadyeremo ana ankhosawo.
8 Adzawotche nyamayo ndi kudya usiku womwewo, ndipo adzayidye ndi buledi wophikidwa popanda yisiti pamodzi ndi masamba wowawa.
9 Musadzadye yayiwisi kapena yophika, koma mudzawotche yonse, mutu, miyendo ndi zamʼmimba.
10 Musadzasiye nyama ina mpaka mmawa, ngati ina idzatsala mpaka mmawa, mudzayitenthe.
11 Muzidzadya nyamayo mutavala chotere, pokonzekera ulendo: mudzazimangirire lamba mʼchiwuno, nsapato zanu kuphazi ndi ndodo yanu kumanja. Mudzadye mofulumira. Imeneyi ndi Paska ya Yehova.
12 “Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova.
13 Magazi amene mudzawaze pa mphuthu za zitseko ndi pamwamba pa zitseko aja adzakhala ngati chizindikiro. Ine ndikadzaona magaziwo ndidzakudutsani, ndipo ndikadzamakantha anthu a Igupto, mliri wosakazawu sudzakukhudzani.
14 “Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova.
15 Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti. Tsiku loyamba muzichotsa yisiti mʼnyumba zanu, ngati aliyense adzadya kanthu kalikonse kali ndi yisiti kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzayenera kuchotsedwa mʼgulu la Israeli.
16 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika, ndipo winanso uzikhala pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Musamagwire ntchito masiku onsewa, koma ntchito yokonza chakudya yokha kuti aliyense adye. Izi ndi zimene muzichita.
17 “Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa ndi pa tsiku limeneli ndinatulutsa magulu anu mʼdziko la Igupto. Muzikondwerera tsiku limeneli pa mibado yonse ngati lamulo lamuyaya.
18 Mwezi woyamba muzidzadya buledi wopanda yisiti kuyambira madzulo tsiku la 14 la mweziwo mpaka tsiku la 21 mwezi womwewo.
19 Yisiti asamapezeka mʼnyumba zanu kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo aliyense amene adya chakudya chimene muli yisiti, munthu ameneyo ayenera kuchotsedwa mʼgulu la Aisraeli, kaya iyeyo ndi mlendo kapena mbadwa.
20 Musadye chilichonse chokhala ndi yisiti. Kulikonse kumene mukukhala, muyenera kudya buledi wopanda yisiti.”
21 Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, “Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska.
22 Mutengenso nthambi ya chitsamba cha hisope, muchiviyike mʼmagazi amene mwawayika mʼbeseni ndipo muwaze ena mwa magaziwo pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko. Palibe aliyense wa inu amene adzatuluke mʼnyumba yake mpaka mmawa.
23 Pamene Yehova adzadutsa mʼdziko kudzakantha Aigupto, nʼkuona magazi pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko, Iye adzadutsa khomo limenelo ndipo sadzalola woonongayo kuti alowe mʼnyumba zanu kuti akukantheni.
24 “Muzimvera malamulo amenewa kwa muyaya, inu ndi zidzukulu zanu.
25 Mukakalowa mʼdziko limene Yehova adzakupatseni monga analonjeza, mukasunge mwambo umenewu.
26 Ndipo ana anu akakakufunsani kuti, ‘Mwambo umenewu ukutanthauza chiyani?’
27 Inu mukawawuze kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’ ” Kenaka anthu anawerama napembedza.
28 Aisraeli anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.
29 Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo.
30 Farao ndi nduna zake zonse ndiponso Aigupto onse anadzuka pakati pa usiku, ndipo kunali kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, pakuti panalibe nyumba imene munalibe munthu wakufa.
Kutuluka kwa Aisraeli
31 Pakati pa usiku Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Nyamukani! Asiyeni anthu anga, inu ndi Aisraeli! Pitani, kapembedzeni Yehova monga munapempha.
32 Tengani ziweto ndi ngʼombe zanu ndipo pitani kapembedzeni Mulungu wanu monga munanenera kuti ine ndidalitsike.”
33 Aigupto anawawumiriza anthuwo kuti atuluke mofulumira ndi kusiya dziko lawo. Iwo anati, “Ngati sitiwalola kutero, tonse tidzafa.”
34 Motero anthuwo ananyamula ufa wawo wopangira buledi asanathiremo yisiti ndipo anasenza pa mapewa awo pamodzi ndi zokandiramo buledi atazikulunga mu nsalu.
35 Aisraeli anachita monga anawawuzira Mose kuti apemphe kwa Aigupto zozikongoletsera zasiliva ndi zagolide ndi zovala.
36 Yehova anafewetsa mtima Aigupto kuti akomere mtima Aisraeliwo ndipo anawapatsa zimene anawapempha. Motero Aisraeli anawalanda zinthu Aigupto.
37 Aisraeli anayenda ulendo kuchokera ku Ramesesi mpaka kukafika ku Sukoti. Anthu aamuna oyenda pansi analipo 600,000 osawerengera akazi ndi ana.
38 Anthu enanso ambiri anapita nawo, kuphatikizanso gulu lalikulu la ziweto, mbuzi, nkhosa pamodzi ndi ngʼombe.
39 Iwo anapanga buledi wopanda yisiti ndi ufa umene anachoka nawo ku Igupto. Ufawo unalibe yisiti chifukwa anachita kuthamangitsidwa ku Igupto ndipo analibe nthawi yokonzera chakudya chawo.
40 Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430.
41 Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto.
42 Usiku wonse Yehova anachezera kutulutsa ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake pa tsiku limeneli Aisraeli onse azichezera usiku wonse kulemekeza Mulungu kamba ka mibado yonse ya mʼtsogolo.
Lamulo la Paska
43 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Malamulo a Paska ndi awa:
“Mlendo asadye Paska.
44 Kapolo aliyense amene munagula angadye ngati atayamba wachita mdulidwe.
45 Koma amene mukukhala naye kwa kanthawi kapena waganyu asadye Paska.
46 “Muzidyera Paska mʼnyumba imodzi. Musatulutse nyama iliyonse kunja kwa nyumba. Musaswe mafupa aliwonse.
47 Gulu lonse la Israeli lizichita mwambo wachikondwererochi.
48 “Ngati mlendo wokhala pakati panu angafune kuchita nawo mwambo wa chikondwerero cha Paska, cha Yehovachi, amuna onse a mʼnyumba mwake ayenera kuchita mdulidwe. Akatero muzimutenga ngati mbadwa pakati panu. Koma aliyense wosachita mdulidwe asadye Paska.
49 Lamulo limeneli likhudza mbadwa ngakhalenso alendo wochita mdulidwe wokhala pakati panu.
50 “Aisraeli onse anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.
51 Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.”