5
Ufulu mwa Khristu
1 Khristu anatimasula kuti tikhale mfulu. Tsono chirimikani, ndipo musakodwenso mʼgoli la ukapolo.
2 Chonde mvetsetsani! Ine Paulo, ndikukuwuzani kuti mukalola kuchita mdulidwe, Khristu simupindula nayenso konse.
3 Ndikubwerezanso kuwuza munthu aliyense wovomereza kuchita mdulidwe kuti ayeneranso kutsata Malamulo onse.
4 Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo.
5 Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza.
6 Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.
7 Inu munkathamanga mpikisano wanu wabwino. Anakuletsani ndani kuti musamverenso choonadi?
8 Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Iye amene anakuyitanani.
9 “Yisiti wapangʼono amagwira ntchito mu buledi yense.”
10 Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani.
11 Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa.
12 Kunena za amene akukuvutani, ndikanakonda akanangodzithena okha!
Moyo mwa Mzimu Woyera
13 Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi.
14 Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”
15 Ngati mupitiriza kulumana ndi kukhadzulana, samalani kuti mungawonongane.
16 Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo.
17 Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna.
18 Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo.
19 Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa;
20 kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko
21 ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.
22 Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
23 kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
24 Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo.
25 Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.
26 Tisakhale odzitukumula, oputana ndi ochitirana nsanje.