27
Yakobo Alandira Madalitso kwa Isake
1 Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.”
Iye anayankha, “Ine abambo.”
2 Isake anati, “Tsopano ine ndakalamba, ndipo sindidziwa tsiku langa lakufa.
3 Tsono tenga zida zako, muvi wako ndi uta, pita kuthengo ukandiphere nyama.
4 Undikonzere chakudya chabwino monga muja ndimakonderamu ndipo ubwere nacho kwa ine kuti ndidye ndi kuti ndikudalitse ndisanamwalire.”
5 Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama,
6 Rebeka anati kwa mwana wake Yakobo, “Taona ndamva abambo ako akuwuza mʼbale wako Esau kuti,
7 ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’
8 Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze:
9 Pita ku khola, ukatenge ana ambuzi abwino awiri, kuti ndikonzere abambo ako chakudya chokoma monga amakondera.
10 Kenaka upite nacho chakudyacho kwa abambo ako kuti adye ndi kukudalitsa asanafe.”
11 Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala.
12 Mwina abambo anga adzandikhudza, ndipo ndidzaoneka kuti ndawapusitsa. Tsono ndizadzitengera temberero mʼmalo mwa madalitso.”
13 Amayi ake anati kwa iye, “Mwana wanga, temberero limenelo ligwere ine. Iwe ungochita zimene ine ndikukuwuza; pita kanditengere timbuzito.”
14 Choncho anapita nakatenga timbuzito ndi kubwera nato kwa amayi ake. Choncho Rebeka anaphika chakudya chokoma monga momwe Isake amakondera.
15 Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo.
16 Anamuvekanso manja ake ndi khosi lake ndi zikopa za mwana wambuzi.
17 Kenaka, anamupatsa Yakobo chakudya chokoma chija chimene anaphika pamodzi ndi buledi.
18 Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.”
Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?”
19 Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.”
20 Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?”
Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”
21 Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.”
22 Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.”
23 Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa.
24 Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?”
Yakobo anayankha, “Inde ndine.”
25 Ndipo iye anati, “Mwana wanga, patseko nyama yakoyo ndidye kuti ndikudalitse.”
Yakobo anabwera ndi nyama ija kwa Isake ndipo anadya. Kenaka anamupatsanso vinyo ndipo anamwa.
26 Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.”
27 Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati,
“Haa, fungo la mwana wanga
lili ngati fungo la munda
umene Yehova waudalitsa.
28 Mulungu akugwetsere mame akumwamba
ndipo minda yako ibale tirigu wambiri
ndi vinyo watsopano.
29 Mitundu ya anthu ikutumikire iwe
ndipo anthu akugwadire iwe.
Ukhale wolamula abale ako,
ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire.
Amene akutemberera iwe atembereredwe
ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”
30 Isake atatsiriza kudalitsa Yakobo, atangochoka pamaso pa abambo akewo, Esau anabwera kuchokera kosaka kuja.
31 Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.”
32 Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?”
Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”
33 Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”
34 Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!”
35 Koma iye anati, “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo ndipo watenga madalitso ako.”
36 Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”
37 Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?”
38 Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.
39 Tsono Isake abambo ake anamuyankha kuti,
“Malo ako okhalapo
sadzabala dzinthu,
ndipo mvula sidzagwa pa minda yako.
40 Udzakhala ndi moyo podalira lupanga
ndipo udzatumikira mʼbale wako.
Koma idzafika nthawi
pamene udzakhala mfulu
udzachotsa goli lake mʼkhosi mwako.”
Yakobo Athawira kwa Labani
41 Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.”
42 Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, “Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire.
43 Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani.
44 Ukakhale naye kwa kanthawi mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utatsika.
45 Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?”
46 Tsono Rebeka anati kwa Isake, “Ine sindikukondwera nawo anamwali a Chihiti. Ndipo ngati Yakobo angapeze mbeta kuno mwa anamwali a Chihitiwa, ndiye kuli bwino kungofa.”