14
Kulapa Kubweretsa Madalitso
Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.
Machimo anu ndi amene akugwetsani!
Bweretsani zopempha zanu
ndipo bwererani kwa Yehova.
Munene kwa Iye kuti,
“Tikhululukireni machimo athu onse
ndi kutilandira mokoma mtima,
kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
Asiriya sangatipulumutse;
ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,
sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’
kwa zimene manja athu omwe anazipanga,
pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”
 
Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo
ndipo ndidzawakonda mwaufulu
pakuti ndaleka kuwakwiyira.
Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli
Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.
Adzazika mizu yake pansi
ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
mphukira zake zidzakula.
Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,
kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.
Iye adzakula bwino ngati tirigu.
Adzachita maluwa ngati mphesa
ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.
Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?
Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.
Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;
zipatso zako zimachokera kwa Ine.”
 
Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.
Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.
Njira za Yehova ndi zolungama;
anthu olungama amayenda mʼmenemo,
koma anthu owukira amapunthwamo.