10
1 Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo,
kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,
2 kuwalanda anthu osauka ufulu wawo
ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga,
amalanda zinthu za akazi amasiye
ndi kubera ana amasiye.
3 Kodi mudzatani pa tsiku la chilango,
pofika chiwonongeko chochokera kutali?
Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni?
Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
4 Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa
kapena kufa pamodzi ndi ophedwa.
Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere,
mkono wake uli chitambasulire.
Chiweruzo cha Mulungu pa Asiriya
5 “Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga,
iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!
6 Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu,
ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine,
kukafunkha ndi kulanda chuma,
ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.
7 Koma izi si zimene akufuna kukachita,
izi si zimene zili mʼmaganizo mwake;
cholinga chake ndi kukawononga,
kukapulula mitundu yambiri ya anthu.
8 Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’
9 ‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi?
Kodi Hamati sali ngati Aripadi,
nanga Samariya sali ngati Damasiko?
10 Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano,
mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;
11 nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake
monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’ ”
12 Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake.
13 Pakuti mfumuyo ikuti,
“ ‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa,
ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu.
Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu,
ndinafunkha chuma chawo;
ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.
14 Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu
ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame,
ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa,
motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse;
palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake,
kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”
15 Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito,
kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito?
Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula,
kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!
16 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu;
kunyada kwa mfumuyo kudzapsa
ndi moto wosazima.
17 Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto,
Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto.
Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza
ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
18 Ankhondo ake adzawonongedwa
ngati nkhalango yayikulu
ndi ngati nthaka yachonde.
19 Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri,
yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.
Aisraeli Otsala
20 Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli,
opulumuka a nyumba ya Yakobo,
sadzadaliranso anthu
amene anawakantha,
koma adzadalira Yehova,
Woyerayo wa Israeli.
21 Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo
adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.
22 Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja,
otsala okha ndiwo adzabwerere.
Chiwonongeko chalamulidwa,
chidzaonetsa chilungamo chosefukira.
23 Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse
monga momwe analamulira.
24 Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti,
“Inu anthu anga okhala mu Ziyoni,
musawaope Asiriya,
amene amakukanthani ndi ndodo
nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
25 Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu
ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”
26 Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu,
monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu;
ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi
ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
27 Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu,
goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu;
golilo lidzathyoka
chifukwa cha kunenepa kwambiri.
28 Adani alowa mu Ayati
apyola ku Migironi;
asunga katundu wawo ku Mikimasi.
29 Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti,
“Tikagona ku Geba”
Rama akunjenjemera;
Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.
30 Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu!
Tchera khutu, iwe Laisa!
Iwe Anatoti wosauka!
31 Anthu a ku Madimena akuthawa;
anthu a ku Gebimu bisalani.
32 Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu;
adzagwedeza mikono yawo,
kuopseza anthu a ku Ziyoni,
pa phiri la Yerusalemu.
33 Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,
adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo,
mitengo yodzikweza idzadulidwa,
mitengo yayitali idzagwetsedwa.
34 Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira;
Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.