35
Chimwemwe cha Opulumutsidwa
1 Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala;
dziko lowuma lidzakondwa
ndi kuchita maluwa.
2 Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka
lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe.
Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni,
maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni.
Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova,
ukulu wa Mulungu wathu.
3 Limbitsani manja ofowoka,
limbitsani mawondo agwedegwede;
4 nenani kwa a mitima yamantha kuti;
“Limbani mtima, musachite mantha;
Mulungu wanu akubwera,
akubwera kudzalipsira;
ndi kudzabwezera chilango adani anu;
akubwera kudzakupulumutsani.”
5 Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso
ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
6 Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala,
ndipo osayankhula adzayimba mokondwera.
Akasupe adzatumphuka mʼchipululu
ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
7 mchenga wotentha udzasanduka dziwe,
nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe.
Pamene panali mbuto ya ankhandwe
padzamera udzu ndi bango.
8 Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu;
ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika.
Anthu odetsedwa
sadzayendamo mʼmenemo;
zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
9 Kumeneko sikudzakhala mkango,
ngakhale nyama yolusa sidzafikako;
sidzapezeka konse kumeneko.
Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
10 Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera.
Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba;
kumeneko adzakondwa mpaka muyaya.
Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe,
ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.