20
Yeremiya ndi Pasuri
1 Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi.
2 Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova.
3 Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse.
4 Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo.
5 Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni.
6 Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ”
Madandawulo a Yeremiya
7 Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi;
Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana.
Anthu akundinyoza tsiku lonse.
Aliyense akundiseka kosalekeza.
8 Nthawi iliyonse ndikamayankhula,
ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka!
Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka
ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse.
9 Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye
kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,”
mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga,
amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga.
Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa,
koma sindingathe kupirirabe.
10 Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti,
“Zoopsa ku mbali zonse!
Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!”
Onse amene anali abwenzi anga
akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti,
“Mwina mwake adzanyengedwa;
tidzamugwira
ndi kulipsira pa iye.”
11 Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu.
Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana.
Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana.
Manyazi awo sadzayiwalika konse.
12 Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama
ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu.
Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga
popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.
13 Imbirani Yehova!
Mutamandeni Yehova!
Iye amapulumutsa wosauka
mʼmanja mwa anthu oyipa.
14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!
Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!
15 Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga
ndi uthenga woti:
“Kwabadwa mwana wamwamuna!”
16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene
Yehova anayiwononga mopanda chisoni.
Amve mfuwu mmawa,
phokoso la nkhondo masana.
17 Chifukwa sanandiphere mʼmimba,
kuti amayi anga asanduke manda anga,
mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.
18 Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni
kuti moyo wanga
ukhale wamanyazi wokhawokha?