23
Nthambi Yolungama
1 “Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova.
2 Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova.
3 “Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana.
4 Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.
5 Yehova akuti, “Masiku akubwera,
pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka.
Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
6 Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka
ndipo Israeli adzakhala pamtendere.
Dzina limene adzamutcha ndi ili:
Yehova ndiye Chilungamo Chathu.
7 Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’
8 koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
Aneneri Onyenga
9 Kunena za aneneri awa:
Mtima wanga wasweka;
mʼnkhongono mwati zii.
Ndakhala ngati munthu woledzera,
ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo,
chifukwa cha Yehova
ndi mawu ake opatulika.
10 Dziko ladzaza ndi anthu achigololo;
lili pansi pa matemberero.
Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma.
Aneneri akuchita zoyipa
ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
11 “Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova.
Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,”
akutero Yehova.
12 “Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera;
adzawapirikitsira ku mdima
ndipo adzagwera kumeneko.
Adzaona zosaona
mʼnthawi ya chilango chawo,”
akutero Yehova.
13 “Pakati pa aneneri a ku Samariya
ndinaona chonyansa ichi:
Ankanenera mʼdzina la Baala
ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
14 Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu
ndaonapo chinthu choopsa kwambiri:
amachita chigololo, amanena bodza
ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa.
Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake.
Kwa Ine anthu onsewa
ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
15 Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ndidzawadyetsa zakudya zowawa
ndi kuwamwetsa madzi a ndulu,
chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse
ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu;
zomwe aloserazo nʼzachabechabe.
Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi,
osati zochokera kwa Yehova.
17 Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti,
‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’
Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti,
‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”
18 Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova?
Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake?
Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
19 Taonani ukali wa Yehova
uli ngati chimphepo chamkuntho,
inde ngati namondwe.
Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
20 Mkwiyo wa Yehova sudzaleka
mpaka atachita zonse zimene
anatsimikiza mu mtima mwake.
Mudzazizindikira bwino zimenezi
masiku akubwerawa.”
21 Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa,
komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo;
Ine sindinawayankhule,
komabe iwo ananenera.
22 Iwo akanakhala pa msonkhano wanga
ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga.
Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa
kuti aleke machimo awo.”
23 Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,
ndiye sindine Mulungu?
24 Kodi wina angathe kubisala
Ine osamuona?”
“Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”
Akutero Yehova.
25 “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’
26 Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo.
27 Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala.
28 Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga?
29 Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
30 Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.”
31 Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ”
32 Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
Uthenga Wabodza ndi Aneneri Abodza
33 Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’
34 Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake.
35 Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’
36 Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.
37 Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’
38 Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule,
39 ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu.
40 Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”