30
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
1 Yehova anawuza Yeremiya kuti,
2 “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndakuwuza.
3 Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”
4 Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda:
5 “Yehova akuti:
“Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa,
ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.
6 Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti:
Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana?
Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna
atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira?
Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
7 Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri!
Sipadzakhala lina lofanana nalo.
Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo,
koma adzapulumuka ku masautsowo.”
8 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo,
ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo
ndipo ndidzadula zingwe zowamanga;
Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.
9 Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo
ndiponso Davide mfumu yawo,
amene ndidzawasankhira.
10 “ ‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo;
usade nkhawa, iwe Israeli,’
akutero Yehova.
‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali,
zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo.
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere,
ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha.
11 Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’
akutero Yehova.
‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu
kumene ndinakubalalitsirani,
koma inu sindidzakuwonongani kotheratu.
Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa.
Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ”
12 Yehova akuti,
“Chilonda chanu nʼchosachizika,
bala lanu ndi lonyeka.
13 Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu,
palibe chiyembekezo choti inu nʼkuchira,
palibe mankhwala ochiritsa inu.
14 Abwenzi anu onse akuyiwalani;
sasamalanso za inu.
Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira.
Ndipo ndakulangani mwa nkhanza,
chifukwa machimo anu ndi ambiri,
ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
15 Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu?
Bala lanu silingapole ayi.
Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri
ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.
16 “Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa;
adani anu onse adzapita ku ukapolo.
Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso;
onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.
17 Ndidzachiza matenda anu
ndi kupoletsa zilonda zanu,
akutero Yehova,
‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika.
Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”
18 Yehova akuti,
“Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo
ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo;
mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake,
nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
19 Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova
ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo.
Ndidzawachulukitsa,
ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika;
ndidzawapatsa ulemerero,
ndipo sadzanyozedwanso.
20 Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale,
ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga;
ndidzalanga onse owazunza.
21 Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo.
Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo.
Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira.
Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane
popanda kuyitanidwa?”
akutero Yehova.
22 “Choncho inu mudzakhala anthu anga,
ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”
23 Taonani ukali wa Yehova wowomba
ngati mphepo ya mkuntho.
Mphepo ya namondwe
ikuwomba pa mitu ya anthu oyipa.
24 Mkwiyo woopsa wa Yehova sudzachoka
mpaka atakwaniritsa zolinga
za mu mtima mwake.
Mudzamvetsa zimenezi
masiku akubwerawo.