43
1 Yeremiya atatsiriza kuwawuza anthuwo mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova anamutuma kuti akawawuze,
2 Azariya mwana wa Hosayia ndi Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi anthu onse odzikuza anawuza Yeremiya kuti, “Ukunama iwe! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti unene kuti, ‘Musapite ku Igupto kukakhala kumeneko.’
3 Koma ndi Baruki mwana wa Neriya amene akukulimbikitsa kuti utiletse zopita ku Igupto ndi kuti mʼmalo mwake tidzipereke mʼmanja mwa Ababuloni, kuti iwo atiphe kapena kutitenga ukapolo ku Babuloni.”
4 Motero Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi anthu onse sanamvere lamulo la Yehova loti akhale mʼdziko la Yuda.
5 Mʼmalo mwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo anatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene anabwera kudzakhala mʼdziko la Yuda kuchokera ku mayiko onse kumene anabalakirako.
6 Mʼgulu la anthu otengedwalo munali amuna onse, akazi ndi ana, ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anawasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani pamodzinso ndi mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya.
7 Kotero anthuwo analowa mʼdziko la Igupto chifukwa anakana kumvera Yehova, nakafika ku Tapanesi.
8 Ndipo Yehova anayankhula ndi Yeremiya ku Tapanesi kuti,
9 “Tenga miyala inayi yayikulu ndipo uyikwirire mʼdothi pa chiwundo cha polowera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Uchite zimenezi Ayuda onse akuona.
10 Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayitana mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzakhazika mpando wake waufumu pa miyala imene ndayikwirira apayi. Iye adzafunyulula tenti yake yaufumu pa miyala imeneyi.
11 Iye adzabwera kudzathira nkhondo Igupto. Iwo oyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri, iwo oyenera kutengedwa ukapolo adzatengedwa ukapolo, ndipo iwo oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.
12 Adzayatsa moto mʼnyumba zopembedzera milungu ya Igupto. Adzayeretsa dziko la Igupto monga momwe mʼbusa amayeretsera chovala chake pochotsamo nsabwe. Pambuyo pake adzachoka mʼdziko la Igupto mwa mtendere.
13 Ku Iguptoko adzagwetsa zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzera mulungu wa dzuwa. Adzatentha ndi moto nyumba za milungu ya ku Igupto.’ ”