14
Ahiya Anenera za Kugwa kwa Yeroboamu
1 Pa nthawi imeneyo Abiya mwana wa Yeroboamu anayamba kudwala,
2 ndipo Yeroboamu anati kwa mkazi wake, “Nyamuka ndipo udzibise kuti usadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yeroboamu, ndipo upite ku Silo. Kumeneko kuli mneneri Ahiya amene anandiwuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthu awa.
3 Utenge buledi khumi, makeke ndiponso botolo la uchi ndipo upite kwa mneneriyo. Iye adzakuwuza zimene zidzamuchitikire mwanayu.”
4 Choncho mkazi wa Yeroboamu anadzibisa ndipo anapita ku nyumba ya Ahiya ku Silo.
Tsono Ahiya sankatha kupenya bwino. Ankangoona kuti mbuu chifukwa cha ukalamba.
5 Koma Yehova nʼkuti atamuwuza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yeroboamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake pakuti akudwala, ndiye udzamuyankhe zakutizakuti mkaziyo. Iye akafika, adzadzibisa.”
6 Tsono Ahiya atamva mgugu wa mapazi ake pa khomo, anati, “Lowa, iwe mkazi wa Yeroboamu. Bwanji ukudzibisa? Ine ndatumidwa kuti ndikuwuze nkhani yoyipa.
7 Pita, kamuwuze Yeroboamu kuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakukweza pakati pa anthu ndipo ndinakuyika kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli.
8 Ndinachotsa ufumu ku nyumba ya Davide ndi kuwupereka kwa iwe, koma iwe sunafanane ndi mtumiki wanga Davide, amene ankasunga malamulo anga ndi kunditsata Ine ndi mtima wake wonse, kuchita zolungama zokhazokha pamaso panga.
9 Ndipo iwe wachita zoyipa kupambana onse amene analipo kale. Wadzipangira milungu ina, mafano a zitsulo. Iweyo wandikwiyitsa ndipo wandiwukira.
10 “ ‘Choncho taona, ndidzabweretsa masautso pa nyumba ya Yeroboamu. Ndipo ndidzawononga munthu wamwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yemwe mʼdziko la Israeli. Ndidzatentha nyumba ya Yeroboamu monga mmene munthu amatenthera ndowe mpaka yonse kutheratu.
11 Agalu adzadya aliyense wa banja la Yeroboamu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame zamlengalenga zidzadya iwo amene adzafere ku thengo, pakuti Yehova watero!’
12 “Ndipo iwe nyamuka, bwerera ku nyumba kwako. Phazi lako likadzangoponda mu mzindamo, mwanayo adzamwalira.
13 Aisraeli onse adzalira maliro ake ndi kumuyika mʼmanda. Ndi yekhayo wa banja la Yeroboamu amene adzayikidwe mʼmanda, pakuti ndi mwa iye yekha mmene Yehova Mulungu wa Israeli wapezamo kanthu kabwino.
14 “Koma Yehova adzadzisankhira yekha mfumu yolamulira Israeli imene idzawononga banja la Yeroboamu. Tsiku lake ndi lero! Ndati chiyani? Inde, ndi lero lomwe lino.
15 Ndipo Yehova adzakantha Israeli, kotero kuti adzakhala ngati bango logwedera pa madzi. Iye adzazula Israeli mʼdziko labwino limene analipereka kwa makolo ake ndi kuwamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa anakwiyitsa Yehova pamene anapanga mafano a Asera.
16 Ndipo Iye sadzasamalanso Israeli chifukwa cha machimo amene anachita Yeroboamu ndi kuchimwitsa nawo Israeli.”
17 Tsono mkazi wa Yeroboamu anayimirira nachoka kupita ku Tiriza. Atangoponda pa khonde la nyumba yake, mwana uja anamwalira.
18 Aisraeli anamuyika mʼmanda, ndipo onse analira maliro ake, monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya.
19 Ntchito zina pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu, nkhondo zake ndi mmene ankalamulirira zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
20 Iye analamulira zaka 22 ndipo anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Nadabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Rehobowamu Mfumu ya Yuda
21 Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya ku Yuda. Iye analowa ufumu ali ndi zaka 41, ndipo analamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anawusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti ayikemo Dzina lake. Amayi ake anali Naama, wa ku Amoni.
22 Anthu a ku Yuda anachita zoyipa pamaso pa Yehova kupambana mmene anachitira makolo awo ndipo Yehova anawakwiyira.
23 Iwonso anadzipangira malo opembedzerapo mafano pa chitunda chilichonse ndi kuyimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya Asera pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
24 Mʼdzikomo munalinso amuna ochita zachiwerewere mwa chipembedzo. Anthu ankachita zonyansa zonse za anthu a mitundu ina imene Yehova anayipirikitsa asanafike Aisraeli.
25 Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisaki, mfumu ya Igupto, anadzathira nkhondo Yerusalemu.
26 Ananyamula chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu. Anatenga chilichonse, ngakhalenso zishango zonse zagolide zimene Solomoni anapanga.
27 Ndipo Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zamkuwa mʼmalo mwake, nazipereka mʼmanja mwa olamulira alonda a pa khomo pa nyumba ya mfumu.
28 Nthawi zonse mfumu ikamapita ku Nyumba ya Yehova, alonda ankanyamula zishangozo, kenaka ankazisunga mʼchipinda cha alonda.
29 Tsono ntchito zina za Rehobowamu ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
30 Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu.
31 Ndipo Rehobowamu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Amayi ake anali Naama wa ku Amoni. Ndipo Abiya analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.