3
Atsogoleri ndi Aneneri Adzudzulidwa
Ndipo ine ndinati,
“Tamverani, inu atsogoleri a Yakobo,
inu olamulira nyumba ya Israeli.
Kodi sindinu oyenera kudziwa kuweruza molungama,
inu amene mumadana ndi zabwino ndi kukonda zoyipa;
inu amene mumasenda khungu la anthu anga,
ndipo mumakungunula mnofu pa mafupa awo;
inu amene mumadya anthu anga,
mumasenda khungu lawo
ndi kuphwanya mafupa awo;
inu amene mumawadula nthulinthuli
ngati nyama yokaphika?”
 
Pamenepo adzalira kwa Yehova,
koma Iye sadzawayankha.
Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake
chifukwa cha zoyipa zimene anazichita.
Yehova akuti,
“Aneneri amene
amasocheretsa anthu anga,
ngati munthu wina awapatsa chakudya
amamufunira ‘mtendere;’
ngati munthu wina sawapatsa zakudya
amamulosera zoyipa.
Nʼchifukwa chake kudzakuderani,
simudzaonanso masomphenya,
mdima udzakugwerani ndipo simudzawombezanso.
Dzuwa lidzawalowera aneneriwo, ndipo mdima udzawagwera.
Alosi adzachita manyazi
ndipo owombeza mawula adzanyazitsidwa.
Onse adzaphimba nkhope zawo
chifukwa Mulungu sakuwayankha.”
 
Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu,
ndi Mzimu wa Yehova,
ndi kulungama, ndi kulimba mtima,
kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo,
kwa Israeli za tchimo lake.
Imvani izi, inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo,
inu olamulira nyumba ya Israeli,
inu amene mumadana ndi kuweruza kolungama;
ndipo mumakhotetsa zinthu zonse zolondola;
10 inu amene mukumanga Ziyoni pokhetsa magazi,
ndi Yerusalemu ndi kuyipa kwanu.
11 Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze,
ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire,
ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama.
Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti,
“Kodi Yehova sali pakati pathu?
Palibe tsoka limene lidzatigwere.”
12 Choncho chifukwa cha inu,
Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.