7
Chipsinjo cha Israeli
Tsoka ine!
Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe,
pa nthawi yokolola mphesa;
palibe phava lamphesa loti nʼkudya,
palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.
Anthu opembedza atha mʼdziko;
palibe wolungama ndi mmodzi yemwe amene watsala.
Anthu onse akubisalirana kuti aphane;
aliyense akusaka mʼbale wake ndi khoka.
Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa;
wolamulira amafuna mphatso,
woweruza amalandira ziphuphu,
anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna,
onse amagwirizana zochita.
Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati mtengo waminga,
munthu wolungama kwambiri pakati pawo ndi woyipa kuposa mpanda waminga.
Tsiku limene alonda ako ananena lafika,
tsiku limene Mulungu akukuchezera.
Tsopano ndi nthawi ya chisokonezo chawo.
Usadalire mnansi;
usakhulupirire bwenzi.
Usamale zoyankhula zako
ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.
Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake,
mwana wamkazi akuwukira amayi ake,
mtengwa akukangana ndi apongozi ake,
adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe.
 
Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo,
ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga;
Mulungu wanga adzamvetsera.
Kuuka kwa Israeli
Iwe mdani wanga, usandiseke!
Ngakhale ndagwa, ndidzauka.
Ngakhale ndikukhala mu mdima,
Yehova ndiye kuwunika kwanga.
Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova,
chifukwa ndinamuchimwira,
mpaka ataweruza mlandu wanga
ndi kukhazikitsa chilungamo changa.
Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika;
ndidzaona chilungamo chake.
10 Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi
nadzagwidwa ndi manyazi,
iye amene anandifunsa kuti,
“Ali kuti Yehova Mulungu wako?”
Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga;
ngakhale tsopano adzaponderezedwa
ngati matope mʼmisewu.
 
11 Idzafika nthawi yomanganso makoma anu,
nthawi yokulitsanso malire anu.
12 Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu
kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto,
ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate
ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso
kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
13 Dziko lapansi lidzasanduka chipululu
chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo.
Pemphero ndi Matamando
14 Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza,
nkhosa zimene ndi cholowa chanu,
zimene zili zokha mʼnkhalango,
mʼdziko la chonde.
Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi
monga masiku akale.
 
15 “Ndidzawaonetsa zodabwitsa zanga,
ngati masiku amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto.”
 
16 Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi,
ngakhale ali ndi mphamvu zotani.
Adzagwira pakamwa pawo
ndipo makutu awo adzagontha.
17 Adzabwira fumbi ngati njoka,
ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi.
Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo;
mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu
ndipo adzachita nanu mantha.
18 Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,
amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa
za anthu otsala amene ndi cholowa chake?
Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya
koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
19 Inu mudzatichitiranso chifundo;
mudzapondereza pansi machimo athu
ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
20 Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo,
ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu,
monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu
masiku amakedzana.