Salimo 108
Nyimbo. Salimo la Davide.
Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu;
ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse.
Dzukani, zeze ndi pangwe!
Ine ndidzadzutsa mʼbandakucha.
Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina;
ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina.
Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba;
kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga.
Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba,
ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.
 
Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja
kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:
“Mwachipambano Ine ndidzagawa Sekemu
ndipo ndidzayesa chigwa cha Sukoti.
Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;
Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,
Yuda ndi ndodo yanga yaufumu.
Mowabu ndi mbale yanga yosambiramo
ndidzaponya nsapato zanga pa Edomu;
ndidzafuwula mopambana pa Filisitiya.”
 
10 Ndani adzandifikitsa ku mzinda wotetezedwa?
Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
11 Kodi sindinu Mulungu, Inu amene mwatikana
ndipo simuperekezanso magulu athu ankhondo?
12 Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani,
pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake.
13 Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano,
ndipo adzapondereza pansi adani athu.