Salimo 142
Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.
Ndikulirira Yehova mofuwula;
ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.
Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;
ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.
 
Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,
ndinu amene mudziwa njira yanga.
Mʼnjira imene ndimayendamo
anthu anditchera msampha mobisa.
Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;
palibe amene akukhudzika nane.
Ndilibe pothawira;
palibe amene amasamala za moyo wanga.
 
Ndilirira Inu Yehova;
ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,
gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”
Mverani kulira kwanga
pakuti ndathedwa nzeru;
pulumutseni kwa amene akundithamangitsa
pakuti ndi amphamvu kuposa ine.
Tulutseni mʼndende yanga
kuti nditamande dzina lanu.
 
Ndipo anthu olungama adzandizungulira
chifukwa cha zabwino zanu pa ine.